1 Yapo lidawandikila siku la pwando la Pasaka, Yesu wadajhiwa kuti ndhawi yake yochoka pajhiko lapanjhi ni kupita kwa Atate ya kwana. Kila ndhawi wadaakonda wandhu wake anyiyao ali pajhiko, chimwecho wadaakonda mbaka kuuchocha umoyo wake!
2 Yesu wadali ni oyaluzidwa wake adakhala kudyaa chakudya cha ujhulo. Satana wadathomthila Yuda, mwana wa Simoni, mtima wa kumng'anamuka Yesu. 3 Yesu uku ni wajhiwa kuti Atate ampacha kila kandhu muulamulilo wake, ni kuti wadachoka kwa Amnungu ni kubwela kwa Amnungu. 4 Ndiipo, wadasiya kudya chakudya, wadavula njhalu yake ya kubwalo, wadatenga chitambaa chochangulila ni kujhimanga muchiuno. 5 Ndiipo Yesu wadapungulila majhi mbeseni ni kuyamba kwa kwasambiza oyaluzidwa wake mmyendo ni kwachangula kwa chitambaa icho wadajhimanga. 6 Chimwecho yapo wadafika kwa Petulo, Petulo wadafunjha, "Ambuye simunichuke niine mmyendo?"
7 Ndiipo Yesu wadayangha, "Siuchijhiwa icho nichita chipano, nambho pambuyo siujhiwe."
8 Petulo wadamkambila, "Siunichuka myendo muyaya!"
Yesu wadayangha, "Nikasia kukuchuka siukhalanjho ni mgwilizano ni ine."
9 Simoni Petulo wadamkambila, "Ambuye, nichukeni, osati mmyendo pe nambho ni manja ni mutu wanga."
10 Yesu waadakambila, "Mundhu wakathosamba mthupi walibe haja yosambanjho, nambho wafunika kusamba mmyendo, ndande wathoyela thupi lonjhe. Anyiimwe mwayela, nambho osati mwaonjhe." 11 Yesu wadamjhiwa uyo siwamng'anamuke, nde ndande wadakamba, "Anyiimwe mwayela, nambho osati mwaonjhe."
12 Yapo wadathokwasambiza mmyendo ni kuvalanjho njhalu yake ni kukhalanjho pachakudya, wadaafunjha, "Bwanji, mwayajhiwa yayo nakuchitilani? 13 Anyiimwe munitana Oyaluza ni Ambuye, mwakamba mwauzene ine nde mmeneyo. 14 Chipano, ngati ine nili Ambuye ni Oyaluza wanu, nakuchukani anyiimwe myendo, namwe ifunika muchukane myendo. 15 Nakupachani chifani kuti namwe mchite ngati umo nachitilani ine. 16 Zenedi nikukambilani, mbowa osati wamkulu kumpitilila wamkulu wake, ni mtumwi osati wamkulu kusiyana ni uyo wamtuma. 17 Chipano, ndande mwayajhiwa yaya, Amnungu siakupacheni mwawi mkayachita."
18 "Sinikamba chimwecho kwa mwaonjhe. Naajhiwa anyiyao naasangha. Nambho kuti malembo yakwanile, yayo yakamba, ‘Uyo wadya chakudya changa wang'anamuka kunihundukila.’ 19 Ine nikukambilani vindhu ivi chipano vikali vosachokele, dala yapo siyachokele mkhulupilile kuti, ‘Ine nde mmeneyo.’ 20 Zene nikukambilani, uyo wamlandila uyo wanituma wanilandila ine, ni uyo wanilandila ine wamlandila uyo wanituma."
21 Yapo wadakamba yameneyo, Yesu wedadandaula mumtima, wadakamba popande kubisa, "Zene nikukambilani, mmojhi wanu siwaning'anamuke!"
22 Ndiipo oyaluzidwa wake adapenyana, osakhozeletu kumjhiwa yani uyo wamkamba. 23 Oyaluzidwa mmojhi, uyo Yesu wamamkonda kupunda, wadakhala pafupi ni Yesu. 24 Ndiipo Simoni Petulo wadamfotokozela kwa chizindikilo, "Mfunjhe, wamkamba yani?"
25 Oyaluzidwa mmeneyo, uku wanyikizila chidale cha Yesu, wadamfunjha, "Ambuye, yani uyo siwakung'anamukeni?"
26 Yesu waadayangha, "Uyo sinimpache chibandhu cha bumunda icho sinisunjhe mmbale, nde mwene." Ndipo wadatenga chibandhu cha bumunda, wadachisunjha mmbale, wadampacha Yuda, mwana wa Simoni Isikaliyote. 27 Yuda yapo wadalandila chibandhu chimenecho, satana wadamulowa. Ndipo Yesu wadamkambila, "Ichoufuna kuchita, chichite chisanga!" 28 Nambho padalibe waliyonjhe wa anyiyao adakhala pachakudya uyo wadajhiwa ndande yanji Yesu wadamkambila chimwecho Yuda. 29 Pakuti Yuda wadali wosunga chuma hazina, wina amaghaniza kuti Yesu wamamkambila Yuda waghule ivo vifunikana pa phwando, kapina wakaapache kandhu osauka.
30 Chimwecho Yuda pambuyo polandila chibandhu cha bumunda, wadatuluka kubwalo msanga. Ni idali usiku.
31 Yuda yapo wadachoka, Yesu wadakamba, "Chipano Mwana wa Mundhu wapachidwa ulemelelo, ni Amnungu apachidwa ulemelelo mkati mwake."
32 "Ikakhala ulemelelo wa Mnungu wavunukulidwa kupitila Mwana wa Mundhu, ndiipo nawo Amnungu siauvunukule ulemelelo wa Mwana mkati mwake mwene wake, ni siwachite chimwecho mwamsanga. 33 Wanawanga, nikali namwe kwa ndhawi yochepa pe. Simunifunefune, nambho chipano nikukambilani yayo naakambila achogholeli wa Ayahudi, ‘Uko nipita ine anyiimwe simukhoza kupita!’ 34 Nikupachani lamulo la chipano, ngati umo nakukondelani anyiimwe, namwenjho mkondane mwachinawene kwa mwachinawene. 35 Mkakondana, wandhu onjhe sajhiwe kuti anyiimwe nde oyaluzidwa wanga."
36 Simoni Petulo wadamfunjha Yesu, "Ambuye, mpita kuti?"
Yesu wadayangha, "Uko nipita siukhoza kunichota chipano, nambho siunichote pambuyo."
37 Petulo wadamkambila, "Ambuye, ndande yanji sinikhoza kukuchotani chipano. Ine nili tayali kumwalila ndande yanu!"
38 Yesu wadayangha, "Bwanji, zenedi ulitayali kumwalila ndande ya ine? Uzene nikukambila, tambala wakali osalile, siunikane katatu kuti siunijhiwa."