Publicidade

João 1

Mawu wadachitika thupi

1 Poyamba wadalipo Mawu, nayo wadali ni Amnungu nayo wadali Mnungu. 2 Kuyambila mmayambo Mawu wadali ni Amnungu. 3 Kupitila iye vindhu vonjhe vidaumbidwa, palibe icho chida umbidwa popande iye. 4 Iye wadali chiyambo cha umoyo ni umoyo umenewo udali dangalila kwa wandhu. 5 Dangalila limenelo liwala mumdima, ni mdima siudalikhoze kulithima dangalila limenelo kuti lisawale.

6 Amnungu wadamtuma mundhu mmojhi jhina lake Yohana, 7 uyo wadajha ngati mmboni, kuti walichitile umboni dangalila limenelo kupitila iye wandhu wonjhe akhoze kukhulupilila. 8 Yohana siwadali dangalila mmeneyo, wadajhape kwakambila wandhu nghani za dangalila limenelo. 9 Ili nde lidali dangalila la zene, dangalila ilo likujha pajhiko ni kwawalila wandhu wonjhe.

10 Ndiipo Mawu wadali pajhiko, kwakupitila iye jhiko lidaumbidwa, nambho jhiko silimamjhiwe. 11 Wadajha mujhiko lake mwene, nambho akwake siada mlandile. 12 Nambho anyiyawo adamlandila, nikumkhulupilila mwadapacha nghongono za kukhala wana Amnungu, nde anyiwajha alikhulupilila jhina lawo, 13 anyiyawo abadwa asati kwa mwazi, kapina kwa kukonda kwa thupi au kukonda kwa mundhu, nambho Amnungu nde yawo adali Atate wao.

14 Mawu nalo lidakhala mundhu, ni wadakhala kwathu. Nafe tauona ulemelelo wake, ulemelelo wa Mwana wa yokha wa Atate, wajhala ubwino ni uzene.

15 Yohana wadakambila wandhu nghani za mmeneyo, wadakamba kwa mvekelo, "Uyu nde yujha timamchochela umboni kwakukamba chimwechi, ‘Siwajhe mundhu mmojhi uyo wali wamkulu kusiyana niine, mateyake wadalipo ine nikali osabadwe.’ "

16 Kwakupitila ukwanilicho wake ife tapata ubwino uwo upitilila ubwino woyamba. 17 Pakuti Amnungu wadachocha thauko kwakupitila Musa, nambho ubwino ni uzene vidajha kwa kupitila Yesu Kilisito. 18 Palibe uyo waonapo Amnungu muyaya. Nambho Mwana wao wapayokha uyo walunjana ni Atate, nde uyo wati jhiwicha nghani za Amnungu.

Utenga wa Yohana Mbatizi

19 Uno nde umboni wa Yohana uwo wadauchocha ndhawi iyo achogholeli a Chiyahudi ku Yelusalemu, yapo wadatuma Alawi ni ajhukulu, amfunjhe kuti "Iwe yani?"

20 Yohana siwadakane kwaakambila uzene, popande kubisa, kuti, "Ine osati Kilisito."

21 Ndipo adamfunjha, "Chipano iwe yani? Bwanji, iwe Elia?"

Yohana wadayangha, "Osati ine."

Ndipo adamfunjhanjho, "Bwanji iwe nde yujha mlosi?"

Yohana wadakana, "Notho!"

22 Anyiiwo adamfunjha, "Iwe yani? Tikambile, tikaapache yangho yawo atituma."

23 Yohana wadayangha, "Ine nde yujha uyo mlosi Isaya wadakamba nghani zanga,

‘Mvekelo wa mundhu utana kuphululu.

Konjani njila ya Ambuye.’ "

24 Wandhu anyamenewo adatumidwa ni Afalisayo. 25 Ndiipo, adamfunjha Yohana, "Ngati iwe osati Masiya, kapina Eliya, kapina yujha mlosi, ndande yanji chipano ubatiza?"

26 Yohana wadayangha, "Ine nibatiza kwa majhi, nambho walipo mmojhi, pakati panu, uyo mukali osamjhiwe. 27 Siwajhe pa mbuyo pa ine. Nambho sinikhoza kumasula luzi la malapasi yake."

28 Vindhu vimenevo vidachitika ku Besania, mchija la mchinje Yoludani uko Yohana wamabatizila wandhu.

Mwana wa Mbelele wa Amnungu

29 Mawa lake, Yohana wadamuona Yesu ni wajha kwaiye, wadakamba, "Yuno nde Mwana wa Mbelele wa Amnungu uyo wachocha chimo la wandhu! 30 Uyu nde uyo nimafotokoza nghani zake kuti, ‘Pambuyo panga siwajhe mundhu mmojhi uyo wali wamkulu kupunda kupitilila ine, pakuti wadalipo ine nikali osabadwe.’ 31 Ine namwene sinimamjhiwe, nambho ni batiza kwa majhi kuti wandhu Aizilaeli amjhiwe."

32 Yohana wadachitila umboni chimwechi, "Ni adauona Mzimu niuchika ngati nghunda kuchoka kumwamba ni kutula pa mwamba pake. 33 Ine sinimamjhiwe, nambho uyo wanituma kubatiza wandhu kwa majhi wanikambila, ‘Mundhu uyo siwauone mzimu niuchika kuchoka kumwamba ni kukhala pa mwamba pake, nde uyo wabatiza kwa Mzimu Woyela.’ 34 Ine naona nikuchitila umboni kuti uyu nde Mwana wa Amnungu."

Oyaluzidwa oyamba a Yesu

35 Mawa lake, Yohana wadaimanjho pajha pamojhi ni oyaluzidwa wake awili. 36 Yapo wadamuona Yesu niwapita, wadakamba, "Penyani! Uyu nde Mwana wa Mbelele wa Amnungu."

37 Anyiwajha oyaluzidwa yapo adamvela Yohana ni wakamba mawu yameneyo, adamchata Yesu. 38 Ndiipo, Yesu wadang'anamuka, ni yapo wadaona oyaluzidwa achameneo niamchata, wadafunjha, "Mfunafuna chiyani?"

Anyiiwo adamuyangha, "Oyaluza, mukhala kuti?"

39 Yesu wadatana, "Majhani, namwe simunione." Chimwecho adamchata, ni kupaona pamalo yapo wamakhala, adalongeza naye siku limenelo.

40 Andulea mbale wa Simoni Petulo, wadali mmojhi wa wandhu awili anyiyawo adamvela Yohana niwakamba chimwecho, adamchota Yesu. 41 Pampajha icho wadachita Andulea, wadapezana ni mbale wake, Simoni, wadamkambila, "Tamuona Mesiya" Mateyake Kilisito. 42 Ndiipo, wadampeleka Simoni kwa Yesu.

Chimwecho Yesu wadampenya Simoni nikukamba, "Iwe ni mwana wa Yohana. Chipano siutanidwe Kefa" Pamkambo wa Chighiliki Petulo, mateyake, mwala.

Yesu waatana Filipo ni Nasanaeli

43 Mawa lake, Yesu wadalamula kupita kumujhi wa Galilaya, kumeneko wadampheza Filipo, wadamkambila "Nichate." 44 Filipo wadali mundhu wa kumujhi wa Betisaida, mujhi uwo Petulo ni Andulea amakhala. 45 Filipo yapo wadampheza Nasanaeli, wadamkambila, "Tampheza uyo Musa wadalemba nghani zake muchikalakala cha Thauko, ni uyo alosi adalemba nghani zake, ndekuti Yesu mwana wa Yusufu wa ku Nazaleti."

46 Nasanaeli nayonjho wadamfunjha Filipo, "Bwanji, chindhu cha bwino chikhoza kuchokela ku Nazaleti?"

Ndiipo Filipo wadayangha, "Majha uone."

47 Yesu yapo wadamuona Nasanaeli niwajha kwake, wadakamba nghani zake, "Mmeneyo Muizilaeli mwene. Palibe choipa mkati mwake."

48 Nasanaeli nayonjho wadamfunjha, "Waniona bwanji?"

Yesu wadayangha, "Yapo udali panjhi pa mtengo wa mtini, Filipo wakali osakutane, nidakuona."

49 Ndiipo Nasanaeli wadamkambila, "Oyaluza, imwe ni Mwana wa Amnungu. Imwe ni Amfumu a ku Izilaeli!"

50 Ndiipo Yesu wadafunjha, "Wakhulupilila ndande nakukambila kuti nakuona panjhi pa mtengo wa Mtini? Siuvione vindhu vavikulu kupunda kupitilila ivi." 51 Yesu wadaendekela kukamba, "Nikukambilani uzene, simuone kumwamba nikuvunukuka niatumiki akumwamba Amnungu ni akwela ni kuchika pamwamba pa Mwana wa Amnungu."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-