Publicidade

Marcos 1

Yohana Mbatizi waalalikila wandhu

1 Uwu ni Uthenga Wabwino uwo umuusu Yesu Kilisito, Mwana wa Mnungu. 2 Udayamba ngati umo udalembedwa ni mlosi Isaya,

"Mnungu wadakamba, ‘Sinimtume mthenga wanga wakuchogolele,

uyo siwaikonje njila yako.’

3 Mundhu watana kuchokela kuphululu,

‘Ikonjeni njila ya Ambuye,

mjhikonje kwalandila Ambuye yapo siajhe!’"

4 Chimwecho, mthenga mmeneyo wadali Yohana Mbatizi, wadachokela kuphululu, niwaalalikila wandhu ni kwaabatiza, niwakamba, "Lapani machimo yanu ni kuti mubatizidwe, ni Mnungu siwakulekeleleni machimo yanu." 5 Wandhu ambili amachokela ku jhiko la Yudea ni mmujhi wa Yelusalemu, amapita kumvechela Yohana. Amalapa machimo yao, niiye wamaabatiza mumchinjhe Yolodani.

6 Yohana wadavala chiwalo chidakonjedwa ni mabweya ya chinyama icho chimatanidwa ngamiya, ni lamba la chikwetu mchiuno mwake. Chakudya chake chidali nzige ni uchi wa kuthengo. 7 Yohana wadauzila wandhu, "Mmbuyo mwanga wakujha mundhu uyo wali wamkulu kupitilila ine. Ine sinifunika ata kumasula vingwe va malapasi yake. 8 Ine nikubatizani kwa majhi, nambho iye siwakubatizeni kwa Mzimu Woyela."

Yesu wabatizidwa ni kuyesedwa

9 Ndhawi imeneyo Yesu wadachokela mmujhi wa Nazaleti, mujhiko la Galilaya, wadafika kwa Yohana, nayo wadambatiza mumchinje Yolodani. 10 Yesu yapo wadachuuka mmajhi, pamwepo wadaona kumwamba kwamasulidwa, ni Mzimu Woyela udamchikila ngati nghunda. 11 Mvekelo wa Mnungu udaveka kuchokela kumwamba, niukamba, "Iwe nde mwana wanga uyo nikukonda, nikondelechedwa ni iwe."

12 Pampajha, Mzimu Woyela udamchogoza Yesu kupita kuphululu, 13 wadakhala kumeneko masiku alobaini, niwaesedwa ni Satana. Ni zinyama zamthengo zidali kumeneko, ni atumiki akumwamba a Mnungu adamtumikila.

Yesu waatana alovi anayi amchate

14 Pambuyo pa masiku yambili, Yohana wadamangidwa mndende. Yapo wadali mndende, Yesu wadapita ku Galilaya, wadaalalikila wandhu Uthenga Wabwino wa Mnungu. 15 Wadakamba, "Nyengo ya Mnungu yakwana yolamulila wandhu. Lapani ni kukhulupilila Uthenga Wabwino." 16 Siku limojhi Yesu wamayenda mmbhepete mwanyanja ya Galilaya, wadaaona alovi awili, Simoni ni mphwake Andulea, amatovuwa njhomba. 17 Yesu wadaakambila, "Nichateni, nane sinikuyaluzeni mukhale owapeleka wandhu kwa ine, ngati umo mmavuwila njhomba." 18 Pampajha adavisia vilepa vao nikumchata. 19 Wadapita pachogolo pang'ono, wadaaona Yakobo ni Yohana, wana a Zebedayo. Adakhala mbwato wao, amatotambasula vilepa vawo. 20 Pampajha Yesu yapo wadaona, wadaatana. Anyiiwo adaasiya atate wao a Zebedayo mbwato pamojhi ni wopota njhito wina, adamchata Yesu.

Yesu wamlamicha mundhu wa chiwanda

21 Pambuyo, Yesu ni woyaluzidwa wake adafika mmujhi wa Kapelenaumu. Siku Lopumulila, Yesu wadalowa mnyumba iyo akomanilana Ayahudi, wadayamba kwayaluza wandhu. 22 Wandhu yawo adamvela mayaluzo yake, adazizwa ndande siwamayaluze ngati umo amayaluzila oyaluza athauko la Musa, nambho iye wamayaluza ngati mundhu wa ulamulilo. 23 Pampajha wadatulukila mundhu wachiwanda mujha mnyumba yokomanilana Ayahudi, wadakweza mvekelo waukulu, 24 "Ufuna kutichita chiyani iwe Yesu wa ku Nazaleti? Bwanji, wajha kutipha? Ine nijhiwa kuti iwe ni Woyela, kuchokela kwa Mnungu!" 25 Yesu wadachinyindila chiwanda, "Khala chete! Mchoke mundhu uyu." 26 Chiwanda chimenecho chidamtingiza kwa mbhavu mundhu yujha, chidalila kwa mvekelo waukulu, ni kumchoka. 27 Wandhu wonjhe adazizwa kupunda ni kufunjhana, "Vindhu vanji ivi? Yaya ni mayaluzo ya chipano! Mundhu uyu wali ni ulamulilo wochocha viwanda, navo vimuvela!" 28 Chimwecho, nghani za Yesu zidayenela chisanga mmalo monjhe mwa jhiko la Galilaya.

Yesu waalamicha wandhu ambili

29 Yesu ni oyaluzidwa wake Simoni, ni Anduleya ni Yakobo ni Yohana, adachoka Mnyumba yokomanilana Ayahudi, adapita kukhomo kwa Simoni ni mphwake Anduleya. 30 Apongozi wake waakazi a Simoni, adali agona pachika niadwala homa. Yesu yapo wadafika, adamkambila nghani za wodwala mmeneyo. 31 Yesu wadaasendelela wajhja maye, nikwaagwila jhanja, wadaanyakula. Ni homa idamchoka, wadayamba kwatumikila.

32 Ujhulo yapo udafika, Siku Lopumulila yapo lidatha, wandhu adampelekela Yesu odwala onjhe ni anyiawo adali ni viwanda. 33 Wandhu ambili ammujhi ujha adakomana pa liwala la nyumba. 34 Yesu wadaalamicha wandhu ambili yawo adali ni matenda yosiyana siyana, ni wadavitopola viwanda vambili. Siwadavilole viwanda vikambe, pakuti vimamjhiwa kuti iye ni yani.

Yesu waalalikila wandhu ku jhiko la Galilaya

35 Umawamawa siku lidachatila, Yesu wadapita kubwalo kwa mujhi, pamalo yapo padalibe wandhu, kumeneko wadampembha Mnungu. 36 Simoni ni achanjake adapita kumfunafuna. 37 Yapo adamuona, adamkambila, "Wandhu wonjhe atokufunafuna iwe." 38 Yesu wadaakambila, "Tiyeni ku vijhijhi vina va pafupi. Mmenemo nifunika naalalikile wandhu Uthenga wa Bwino, ndande chimenecho nde icho nachijhela." 39 Chimwecho, Yesu wadapita mmalo yonjhe ya ku jhiko la Galilaya niwaalalikila wandhu mnyumba yokomanilana Ayahudi ni kutopola viwanda.

Yesu wamulamicha mundhu makate

40 Mundhu mmojhi uyo wadali ni makate wadampitila Yesu, wadamgwadila wadampembha, wadakamba, "Ukafuna ukhoza kuniyelecha, kuti nikhoze kumlambila Mnungu!" 41 Yesu wadamlengela lisungu mundhu mmeneyo, wadatambasula jhanja lake ni wadamgafya, kumkambila, "Nifuna, uyelechedwe!" 42 Pampajha makate yadamchoka mundhu mmeneyo, nayo wadalama. 43 Pampajha, Yesu wadamkambila wapite, uku niwamuonya ni wadamkambila, 44 "Siudamkambila mundhu waliyonjhe chindhu ichi, nambho pita ukajhilangize kwa ajhukulu a Mnungu ni ukachoche njhembe ngati umo wadalamulila Musa ni ujhilangize kwa wandhu kuti walama." 45 Nambho mundhu mmeneyo siwadasiye kuuzila nghani zimenezo mmalo yonjhe. Chimwecho Yesu siwadakoze kulowa mmujhi waliwonjhe padanga. Chimwecho Yesu wadakhala pamalo popande wandhu, nambho wandhu amampitila kuchokela kila kumalo.

Veja também

Publicidade
Marcos
Ver todos os capítulos de Marcos
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-22_10-02-25-