Publicidade

Mateus 12

Nghani za siku Lopumulila

1 Ndhawi imeneyo, Yesu wamapita mminda ya mapila siku Lopumulila. Ndiipo oyaluzidwa wake adavela njala, adayamba kupulula ni kufikisa njele za mapila ni kudya. 2 Afalisayo yapo adaona chimwecho, adamkambila Yesu, "Penya, woyaluzidwa wako achita vosaloledwa kuchita Musiku Lopumulila."

3 Yesu wadayangha, "Bwanji, simudasome ivo wadachita Daudi ni achanjake yapo adali ni njala? 4 Iye ni achanjake adalowa Mnyumba ya Mnungu, adadya mabumunda yayo yadachochedwa kwa Mnungu. Iye ni achanjake saadalolezedwe nambho yawo adafunika kudya mabumunda yajha ni ajhukulupe. 5 Simudasome chikalakala cha thauko kuti ajhukulu wakulu awananga thauko pa Siku Lopumulila kwakuchita yajha siyafunika, nambho sadaonekane kuti wolakwa? 6 Chipano nikukambilani, pano wali wamkulu kupitilila Nyumba ya Mnungu. 7 Ngati mdakajhiwa mate ya malembo yaya, ‘Nifuna kulengelena lisungu, osati njhembe yo pyeleza,’ simdakalamula wandhu wosalakwa. 8 Pakuti Mwana wa Mundhu nde Mbuye wa Siku Lopumulila."

Yesu wamlamicha Mundhu ovuwala jhanja

9 Yesu wadachokapo pamalo yajha ni kulowa mnyumba yokomanilana Ayahudi. 10 Mmenemo mdali ni mundhu mmojhi wavulala jhanja. Ndiipo Afalisayo wina adamfunjha Yesu, "Bwanji, ni bwino kumlamicha mundhu Siku Lopumulila?" Adamfunjha chimwecho kuti apate ndande yakumgwilila.

11 Yesu wadaakambila, "Tikambe mmojhi wanu wali ni mbelele iyo yabila mjhenje lonyowa, bwanji siwaichuula mujha mjhenje Siku Lopumulila? 12 Mundhu wali mbasa kupitilila mbelele! Chimwecho tifunika kuchita vindhu vabwino pa Siku Lopumulila." 13 Ndiipo Yesu wadamkambila yujha mundhu, "Tambasula jhanja lako."

Wadatambasula, nalo lidalama ni kukhala ngati jhanja lina lijha. 14 Basi Afalisayo adatuluka kubwalo, ndiipo adafunafuna ndande ya kumphela Yesu.

Mbowa uyo wasanghidwa ni Mnungu

15 Yesu yapo wadajhiwa chindhu chimenecho, wadachoka pamalo pajha. Wandhu ambili adamchata, niiye wadalamicha wandhu wonjhe yawo adali odwala, 16 ndiipo wadalamula kuti sadaakambila wandhu nghani zake. 17 Wadachita chimwecho kuti chijha wadachikamba mlosi Isaya chikwanile,

18 "Uyu nde mbowa wanga uyo namsangha,

uyo nimkonda nikondwelechedwa nayo.

Siniike mzimu wanga mkati mwake,

iye siwalalikile wandhu a mayiko yonjhe lamulo langa.

19 Siwayambana kapina kubula phokoso,

palibe mundhu uyo siwauvele mvekelo wake mnjila.

20 Njhungwi iyo yapindika siwaityola,

wala nyali yofuka mauchi siwaithima,

mbaka kila mundhu walamulidwe ngati umo ifunukila.

21 Wandhu a mayiko yonjhe samkhulupilile iye."

Yesu ni Belizebuli

22 Ndiipo wandhu adampelekela Yesu mundhu osapenya ni uyo siwakhoza kukamba, ndande wadazamwa ni chiwanda. Yesu wadamlamicha, wadakhoza kukamba ni kupenya. 23 Wandhu wonjhe adadabwa ni adakamba, "Bwanji, uyu osati Mwana wa Daudi?"

24 Nambho Afalisayo yapo adavela yameneyo, adakamba, "Mundhu uyu wachocha viwanda kwa mbhavu za Belizebuli, wamkulu wa viwanda."

25 Yesu wadajhiwa maganizo yao, wadakambila, "Ufumu uliwonjhe ukabulana ni ukapatukana magulumagulu, ufumu umenewo siukhoza kulimba. Jhiko kapina wandhu a nyumba imojhi apatukana achinawene magulumagulu yayo yachuchana, nyumba imeneyo siikhoza kulimba. 26 Ngati Satana wamtopola Satana mnjake mmeneyo wajhipatula mwene wake magulumagulu, chimwecho ufumu wake siuime bwanji? 27 Anyiimwe mkamba nichocha chiwanda kwa mbhavu za Belizebuli, bwanji, wana wanu achocha viwanda kwa mbhavu zayani? Kwa ndande imeneyo, achiwanawanu saakulamuleni. 28 Nambho ngati nichocha viwanda kwa mbhavu ya Mzimu wa Mnungu, mujhiwe kuti Ufumu wa Mnungu wathofika kwanu."

29 "Palibe mundhu uyo wakhoza kulowa mnyumba ya mundhu uyo wali ni mbhavu ni kumlanda chuma chake, mbaka poyamba wammange mundhu wa mbhavu yujha. Pamenepo nde yapo siwakhoze kumlanda chuma chake."

30 "Mundhu walionjhe uyo siwali pamojhi ni ine wanichucha ni walionjhe uyo wakana kukusa pamojhi ni ine, mmeneyo watomwaza. 31 Chimwecho nikukambilani, volakwa vonjhe ni chipongwe avichita wandhu saalekeleledwe, nambho yao amchitala chipongwe Mzimu Woyela saalekeleledwa machimo yao. 32 Walionjhe uyo wamtukwana Mwana wa Mundhu siwalekeleledwe, nambho uyo wamtukwana Mzimu Woyela, siwalekeleledwa, kuyambila ndhawi ino mbaka ndhawi ikujha."

Mtengo ni vipacho vake

33 "Mtengo wabwino ubala vipacho vabwino, ni mtengo waopa ubala vipacho voipa. Pakuti mtengo ujhiwika pa vipacho vake. 34 Anyiimwe muli woipa ngati njoka zili ni sumu! Mkhoza bwanji kukamba vindhu vabwino ikakhala mwachinawene wake woipa? Pakuti mundhu wakamba yajha yajhala mumtima mwake. 35 Mundhu wabwino wachocha vindhu vabwino vali mumtima mwake ni mundhu woipa wachocha vindhu voyipa vali mumtima mwake."

36 "Zenedi Nikukambilani, siku la lamulo wandhu siafunike wakambe pa kila mawu loipa ilo alikamba. 37 Pakuti kwa mawu yako siuvomelezeke kuti ni wabwino, ni kwa mawu yako siulamulidwe kuti ni woipa."

Wandhu afuna vizindikilo

38 Ndiipo akumojhi wa oyaluza athauko ni akumojhi a Afalisayo adamkambila Yesu, "Oyaluza, tifuna tione chizindikilo kuchokela kwanu."

39 Yesu wadaayangha, "Mbadwa woipa ni icho chilibe chikhulupililo! Mfuna chizindikilo, nambho simpachidwa chizindikilo nambho chizindikililo chijha cha mlosi Yona. 40 Yona wadakhala masiku ya tatu usiku ni usana mmimba mwa njhomba, nde umo Mwana wa Mundhu siwakhale mkati mwa ndhaka masiku ya tatu usiku ni usana. 41 Wandhu akumujhi wa Ninawi siku la lamulo siaime ni kukupachani mlandu anyiimwe kuti niwolakwa. Pakuti a Ninawi adalapa ndande ya ulaliki wa Yona, chimwecho yapa kuli wamkulu kupitilila Yona! 42 Mfumukazi wa ku Sheba siwaime ndhawi ya lamulo niiye siwakukwilizileni anyiimwe kuti ni wolakwa. Pakuti iye wadamanga ulendo kuchokela mjhiko lake kujha kuvela mawu ya njelu ya Solomoni, ni pano walipo wamkulu kupitilila Solomoni!"

Kubwela kwa chiwanda

43 "Chiwanda chikamchoka mundhu, chizungulila pamalo youma kufunafuna malo yopumulila, ningati sichipata malo, 44 chijhikambila chene, ‘Nibwelele ku nyumba kwanga uko nachoka.’ Nambho pajha chibwela nikuipeza nyumba yopande kandhu, yalambulidwa ni kila chindhu chaikidwa bwino, 45 wachoka ni kupita kutenga viwanda vina saba, voipa kupitilila icho ni wonjhe akujha kumlowa ni kukhala mmememo. Chimwecho umoyo wa mundhu yujha ukhala woipa kupitilila poyamba. Ndeumo siikhalile kwa mbadwa uwu woipa."

Achabale ni amae auzene a Yesu

46 Yesu yapo wadali wakali kukambana ni gulu la wandhu, maye wake ni achabale wake adajha ni kuima kubwalo, naafuna kukamba nayo. 47 Ndiipo mundhu mmojhi wadamkambila, "Maye wako ni achabale wako ali kubwalo, afuna kukambana ni iwe."

48 Yesu wadamuyangha mundhuyo, "Maye wanga ni ayani? Ni achabale wanga ni achiyani?" 49 Ndiipo wadatambasulila jhanja lake ni kwaalangizila oyaluzidwa wake, ni wakamba, "Anyiyawa nde maye wanga ni achabale wanga! 50 Walionjhe uyo wachita vijha avifuna Atate wanga ali kumwamba, mmeneyo nde mbale wanga, ni mlongo wanga ni maye wanga."

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-