1 Yesu yapowadamaliza kwaapacha maagizo oyaluzidwa khumi ni awili, wadachokapo pamenepo, wadapita kuyaluza ni kulalikila wandhu amijhi ya jhiko la Galilaya.
2 Yohana Mbatizi yapo wadali mndende wadavela vindhu ivo wamachita Kilisito. Yohana wadaatuma oyaluzidwa wake akamfunjhe, 3 "Bwanji, iwe nde yujha wadakamba Yohana wakujha, kapina tumlinde mwina?"
4 Yesu wadaayangha, "Pitani ni mkamkambile Yohana yayo mwayaona ni kuyavela. 5 Osapenya apenya, viwete ayenda, amakate alamichidwa, osavela avela, akufa ahyukichidwa ni osauka alalikidwa Uthenga wa Bwino. 6 Ali ni mwawi wandhu yawo sianikhaikila ine."
7 Oyaluzidwa a Yohana yapo amachoka, Yesu wadalifunjha gulu la wandhu nghani za Yohana mbatizi, "Mdapita kuphululu kupenya chiyani? Bwanji, mdafuna kupenya ujhu nilitingizidwa ni mbhepo? 8 Ngati osati chimwecho, chipano mdapita kuona chiyani? Mdapita kumwona mundhu wavala njhalu zabwino? Wandhu yawo avala njhalu zabwino akhala mnyumba za mafumu. 9 Nikambileni, mdapita kupenya chiyani? Bwanji mdapita kumuona mlosi? Notho, nambho mdaona mundhu wamkulu kupitilila mlosi. 10 Uyu nde Yohana uyo wadakambidwa mu Malembo Yoyela niwakamba, ‘Ine, nimtuma mthenga wanga wakuchogolele, uyo siwakukonjele njila.’ 11 Zene nikukambilani, pakati pa wana wonjhe abalidwa ni wamkazi, siwadachokelepo mundhu wa mkulu kupitilila Yohana Mbatizi. Ata chimwecho, yujha wali wamng'ono kupunda mu ufumu wakumwamba ni wamkulu kupitilila Yohana. 12 Kuyambila masiku ya Yohana Mbatizi yapo wamalalikila mbaka lelo, ufumu wa kumwamba uchuchana kwa mbhavu, ni yawo ali ni mbhavu nde yawo aulanda. 13 Thauko la Musa ni mayaluzo yonjhe ya alosi yadakambilila nghani za ufumu wa Mnungu mbaka kujha kwa Yohana Mbatizi. 14 Ngati muvomela, Yohana nde Elia uyo wakadajha. 15 Uyo wali nimakutu yovela, wavele!"
16 "Bwanji wandhu amasiku yano alingana ni chiyani? Alingana ni anyamata yawo akhala paliwala, yawo waatana achanjao ni kwaakambila, 17 ‘Takutimbilani chitolilo, nambho simudavine! Taimba zaya nambho simudalile!’ 18 Yohana wadajha, wadamanga kudya ni kumwa, anyiiwo adakamba, ‘Wazamwa ni chiwanda!’ 19 Mwana wa Mundhu wajha, niwadya ni kumwa, anyiiwo akamba, ‘Mpenyeni uyu waludyo ni olojhela, bwenji wa olandila malipilo ni amachimo!’ Ata chimwecho, njelu ya Mnungu ichimikizidwa zene ndande ya njhito zake."
20 Ndiipo Yesu wadayamba kwaleswa wandhu amijhi iyo wadachita vodabwicha vambili, ndande wandhu wake siadalape. 21 "Uli ni choka iwe Kolazini! Uli ni choka iwe Betisaida! Pakuti, vodabwicha ivo vachitika kwanu vidakachitika ku Tilo ni ku Sidoni, wandhu wake adakalapa ni kuvala maguniya ni kujinyeka vyoso kulangiza kuti alapa machimo yao. 22 Nikukambilani, Mnungu siwakulangeni kupunda anyiimwe kupitilila wandhu amijhi ya Tilo ni Sidoni. 23 Nawe Kapelinaumu, bwanji, uganiza kuti siunyakulidwe mbaka kumwamba? Siuchichidwe mbaka kujhiko la wandhu akufa! Ngati vodabwicha vachitika kwako vidakachitika ku Sodoma, mujhi umeneo udakakhalapo mbaka lelo. 24 Nikukambila, pa siku la lamulo Mnungu siwakulangeni kupunda kupitilila wandhu aku Sodoma."
25 Ndhawi imweyo Yesu wadakamba, "Nikutamandani Atate, Ambuye a kumwamba ni pajhiko, pakuti mwaabisa wandhu anjelu ni wosoma vindu ivi, namwe mwavunukulila wandhu yawo ali ngati wana waang'ono. 26 Yetu, Atate wanga, umu ndeumo mwakondela ichokele."
27 "Atate wanga anipacha vindu vonjhe. Palibe uyo wamjhiwa Mwana nambho Tate wakepe, ni walionjhe yujha Mwana wamsangha kumvunukulila kuti waajhiwe Atate."
28 "Majhani kwa ine, mwaonjhe mchauchika ni kuvutika ni makatundu yolemela, ine sinikuchiteni mpumulile. 29 Jhichocheni kwa ine ni mnitumikile, mujhiyaluze kwanga, pakuti ine asati okalipa ni nilibe mbuli, namwenjho simpumulile. 30 Pakuti, mayaluzo yayo nikupachani asati yolimba ni yopepuka."