1 Kudali mundhu uyo wamatanidwa Ananiya pamojhi ni mkazake uyo watanidwa Safila adagulicha munda wao uwo adalinao. 2 Nambho Ananiya ni mkazake adagwilizana kubisa ndalama yakumojhi, ni kupeleka ndalama izo zidakhalila kwa atumwi. 3 Petulo wadaakambila, "Ananiya, ndande yanji wamulola Satana wakulamulile ni kukuchita umunyenge Mzimu Woyela kwa kubisa ndalama zakumojhi ya izo udagulicha munda? 4 Yapo udali ukali osaghuliche munda udali wako, niyapo udaghulicha ndalama zidalinjho zako ni udakakhoza kutumila ngati umo ufunila iwe. Ndande yanji udaganiza kuchita chimwechi mumtima mwako? Siudamnyenge mundhu, nambho wamnyenga Mnungu." 5 Ananiya yapo wadavela chimwecho, wadagwa panjhi ni kumwalila. Mandha yayakulu yadaapata wandhu wonjhe yawo adavela nghani izo zidachokela. 6 Anyamata adalowa ni kumvinikila sanda thupi lake, adamtulucha kubwalo ni kumzika. 7 Yapo zidatha saa zitatu, mkazake Ananiya wadalowa, osajhiwa icho chachokela. 8 Petulo wadamkambila, "Nikambile, bwanji izi nde ndalama zonjhe izo mudagulicha munda wanu?" Iye wadayangha, "Yetu tidagulicha kwa ndalama zimenezo." 9 Petulo wadamfunjha, "Ndandeyanji muvomelezana kumuyesa Mzimu wa Ambuye? Wandhu yawo amzika mmunako sazino ali pachicheko, nawenjho saapite kukuzika." 10 Ndhawi imweyo Safila wadagwa panjhi ni kumwalila ni mmyendo mwa Petulo. Anyamata wawajha adajha ni adakomana wathokufa, adamtenga ni kupita kumzika pambhepete pa chiliza cha mmunake. 11 Gulu lonjhe, pamojhi ni wandhu wina yawo adavela nghani izi adagwilidwa ni mandha.
12 Atumwi adachita vodabwicha ni vozizwicha vambili pakati pa wandhu. Wandhu adamkhulupilila Yesu wonjhe adakomana kwa pamojhi pa Nyumba ya Amnungu pamalo yapo patanidwa khumbi la Solomoni. 13 Padalibe mundhu mwina waliyonjhe uyo siwamdakhulupilile Yesu wadayesa kulunjana nawo. Ata chimwecho, wandhu wina yawo sadamkhulupilile Yesu wadalemekeza. 14 Nambho chiwelengo cha wandhu yawo adamkhulupilila Ambuye, amachuluka kupunda wachimuna ni waachikazi. 15 Wandhu amajhanawo wodwala ni kwaagoneka pamagodolo ni muvithanda mnjila, kuti ngati ikakhozeka, yapo Petulo siwajhipita, chitunjhi chake chigafye wina wao kuti alame. 16 Gulu la wandhu lidajha kuchokela mmijhi yozungulila Yelusalemu, niajhanawo wodwala wawo ni yawo adazamwa ni viwanda, ni vonjhe adalamichidwa.
17 Ndiipo mjhukulu wa Mkulu ni wonjhe yawo adali pamojhi ni iye, yawo adali agulu la Asadukayo, wadaonela njhanje atumwi, ni kuganiza kwaachitila voipa. 18 Wadaagwila atumwi ni kwaaika mndende. 19 Nambho usiku mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadachekula vicheko va ndende ni kwaatulucha kubwalo, niwakamba, 20 "Pitani mkaime pa nyumba ya Mnungu, mkakambile wandhu mawu yonjhe ya umoyo uno wolunjana ni Yesu." 21 Atumwi wajha yapo adavela yaya, adapita Mnyumba ya Mnungu umawamawa nikuyamba kuyaluza wandhu
Wamkulu wa Ajhukulu ni achanjake yapo adafika, adatana pamojhi msonghano wa bwalo lalikulu la milandu la azee wa a Izilaeli, ni adaatuma wandhu mndende wapelekele wajha atumwi.
22 Nambho alonda wajha yapo adafika kundende, siadampeze atumwi ata mmojhi. Chimwecho adabwelela kwa azee a bwalo la milandu kwaakambila ivo vachitika, 23 adakamba, "Yapo ife tidafika pa ndende, tidapheza vicheko vonjhe vachekedwa ni alonda wonjhe adalipo, nambho yapo tidachekula chicheko, sitidamphezemo mundhu ata mmojhi." 24 Wamkulu wa alonda wa nyumba ya Mnungu ni wamkulu wa ajhembe yapo adavela chimwechi, adagwilidwa ni mandha kupunda, sadajhiwe icho chidachokela. 25 Ndiipo mundhu mmojhi wadajha ni kwaakambila, "Vechalani, wandhu wajha mudaika mndende atuluka ali pa Nyumba ya Mnungu atoyaluza wandhu!" 26 Ndiipo wamkulu wa Nyumba ya Mnungu wadachoka pamojhi ni asikali ni kwaabweza atumwi wajha mndende. Nambho siwadagwile kwa mbhavu ndande adaopa angamenyedwe myala ni wandhu.
27 Basi yapo adaabweza atumwi wajha mndende, wadaalamula kuima pabwalo la milandu. Mjhukulu wamkulu wadaafunjha, 28 "Tidakukanizani kwa mbhavu kuti simudayaluza kupitila jhina la Yesu, nambho penyani icho muchichita! Mwaeneza mayaluzo yanu mujhiko lonjhe la Yelusalemu, ni kufuna kutipacha milandu ya kumpha mundhu mmeneyo."
29 Pamenepo Petulo pamojhi ni atumwi wina adayangha, "Ifunika timvele Mnungu kusiyana ni kwaavela wandhu! 30 Ayiimwe mudampha Yesu pakumpachika pamtanda, nambho Mnungu wa azee wathu wadamuhyukicha. 31 Uyu nde uyo Mnungu wadampacha ulemu ni kumuika kujhanja lake la kwene kuti wakhale mchogoleli ni Muomboli, kuti waapache wandhu a Izilaeli mwawi wolapa ni kulekeleledwa machimo yao. 32 Ife ni amboni a nghani zimenezo, chinchijha ata Mzimu Woyela uyo Mnungu waapacha wandhu wajha amvela wachimikiza chindhu chimenecho."
33 Azee wonjhe a bwalo yapo adavela chimwecho, adakwiiya kupunda mbaka amafuna kuti atumwi aphedwe. 34 Nambho Mfalisayo mmojhi, jhina lake Gamalieli, uyo wadali oyaluza wa thauko ni wadali wolemekezedwa kupunda ni wandhu wonjhe, wadaima pakati pa bwalo. Iye wadalamula atumwi atuluchidwe kubwalo kwa ndhawi yochepa, 35 ndiipo wadalikambila bwalo la azee, "Anyiimwe a Izilaeli anjanga, mjhipenyelele ni yayo mufuna kwaachitila wandhu anyiyawa. 36 Kale wadajha mundhu mmojhi uyo watanidwa Seuda, uyo wadajhichita kuti iye ni mundhu wojhiwika, wadaapata wochatila ngati miya zinayi. Nambho wadaphedwa, ni ochatila wake wonjhe adamwazika ni nghani yake idathela pamenepo. 37 Pambuyo pake wadachokela Yuda wa ku Galilaya ndhawi ya wandhu kuwelengedwa, wadaaguza wandhu ambili kwaiye, nayo wadapedwa, ni wandhu wonjhe yawo adamchata adamwazika. 38 Chipano nikuonyani, mwaasiye wandhu anyiyawa, ngati ganizo lao kapina njhito iyo achita yachokela kwa wandhu, siite yene. 39 Nambho ngati njhito izi zachokela kwa Mnungu, simukhoza kwaakaniza wandhu anyiyawa, mmalo mwake simukhale nimmenyana ni Mnungu."
Wandhu wonjhe adavomelezana ni Gamalieli.
40 Wandhu wajha adavela ivo wadakamba Gamalieli. Wadaatana atumwi wajha mkati, adalamula kuti akwapulidwe mikwapulo, ndiipo wadalamula kuti sadayaluzanjho kwa jhina la Yesu, ndiipo adaasiya ajhipita. 41 Atumwi wajha adatuluka ku bwalo la milandu mujha, uku niakondwa, pakuti Mnungu wadaachita alemekezeke, kwa kwaasiya alenge njhoni ndande ya jhina la Yesu. 42 Kila siku atumwi adaendekele kuyaluza ni kulalika uthenga wabwino pa Nyumba ya Mnungu ni mnyumba za wandhu kuti Yesu nde Kilisito.