1 Ndhawi imweijha Saulo wadayendekela kwaofya ni kupha wandhu yawo amaachata Ambuye. Wadapita kwa mjhukulu wamkulu, 2 ni kumpembha wampache kalata ya kumjhiwicha ku nyumba ya mapembhelo ya Ayahudi ya ku Damasika, kuti wakaapheza wandhu wachimuna kapina wachikazi yao achata mayaluzo ya Yesu, waagwile ni kujhanawo ku Yelusalemu.
3 Mwachizulumukila Saulo yapo wadawandikila pafupi ni mujhi wa ku Damasika, dangalila kuchokela kumlengalenga lidammulika mabendeka yonjhe. 4 Wadagwa panjhi, wadavela mkevelo, "Saulo, Saulo! Ndandeyanji univuticha?"
5 Saulo wadafunjha, "Imwe ayani Ambuye?"
Ujha mvekelo udayangha, "Ine Yesu, uyo umuvuticha. 6 Nambho chipano, nyakuka upite ku mujhi, nawenjho siukambilidwe yayo ufunika kuyachita."
7 Wandhu wajha amayenda pamojhi ni Saulo adangoima popande kukamba mau, adavela mvekelo nambho sadamuone mundhu waliyonjhe uyo wamakamba. 8 Saulo wadaima ni kuphenula maso yake, siwadakhoze kuona kalikonjhe. Chimwecho anjake wajha adamugwila jhanja ni kumchogoza mbaka ku mujhi wa Damasika. 9 Saulo wadakhala siku zitatu popande kupenya, ni pandhawi imeneyo siwadadye kapina kumwa kalikonjhe.
10 Kudali mundhu wokhulupilila mmojhi mu mujhi wa Damasika uyo wamatanidwa Ananiya. Iye wadatanidwa ni Ambuye mumasombhenya, "Ananiya!" Iye wadayangha,
"Ine pano Ambuye!"
11 Ambuye adakamba ni Ananiya, "Ukonjeke upite ku njila iyo itanidwa Njila ya Mojha kwa Mojha, ukafike mnyumba ya Yuda, ukamfunefune mundhu kuchokela ku Taliso, uyo watanidwa Saulo, ni saa zino watopembhela. 12 Saulo wadamuona mundhu mmasombhenya uyo watanidwa Ananiya, niwajha ni kumusanjika manja yake kuti wapenyenjho." 13 Nambho Ananiya wadayangha, "Ambuye, navela nghani zambili kuusu mundhu mmeneyo ni vindhu voipa ivo wadachitila wandhu woyela wako kujha ku Yelusalemu. 14 Nayo wajha kuno ku Damasika ni ulamulilo kuchoka kwa achogoleli a ajhukulu kuti waagwile wandhu wonjhe yawo akhukulupilani imwe."
15 Nambho Ambuye adamuyangha Ananiya, "Pita, pakuti namsangha kuti wanitumikile, walichite jhina langa lijhiwike kwa wandhu osati Ayahudi ni kwa mafumu ni kwa wandhu wonjhe a Izilaeli. 16 Ine namwenewake sinimlangize yambili yayo wafunika kuvutika ndande yanga."
17 Chimwecho Ananiya wadapita, wadalowa mkati umo wadali Saulo ni wadamsanjika jhanja, niwakamba, "Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu yawo adakutulukila panjila, anituma kwako kuti uonenjho ni kujhazidwa Mzimu Woyela." 18 Pomwepo vidagwa vindhu ngati mamba kuchokela mmaso mwake, wadakhoza kuona, wadaima ni wadabatizidwa. 19 Yapo wadathokudya, mbhavu zake zidambwelela.
Saulo wadakhala mumujhi wa Damasika ni wandhu wokhulupilila kwa masiku yochepa. 20 Pampajha wadayamba kulalikila mu nyumba zokamanilana Ayahudi kuti Yesu wadali Mwana wa Mnungu.
21 Wandhu wonjhe yawo adamuvela Saulo adazizwa ni adafunjha, "Uyu osati mundhu yujha wamapha wandhu yawo adamkhulupila Yesu kujha ku Yelusalemu? Ata chimwecho wajha pano kujha kwaagwila wandhu ameneo ni kwaapeleka pachogolo pa waakulu wa ajhukulu?"
22 Nambho mayaluzo ya Saulo yadali ni mbhavu kupunda ni kwadabwicha Ayahudi yawo amakhala mumujhi wa Damasika, umo wadachimikiza kuti Yesu ni Kilisito.
23 Yapo yadatha masiku yambilio, Ayahudi adagwilizana ni adafunafuna njila ya kumupha Saulo, 24 nambho wandhu adamkambila Saulo nghani za mpango wao. Kila siku usana ni usiku amatombisalila mmakomo yonjhe ya mujhi kuti amuphe. 25 Nambho usiku umojhi, wochatila a Saulo adamtenga ni kumuika mumseche ni kumpiticha pandhoolo iyo idali pa phupha la mujhi ni kumchicha mbaka panjhi.
26 Saulo yapo wadafika ku Yelusalemu, wadayesa kulunjana ni atumwi. Nambo onjhe adamuopa, sadakhoze kumkhulupilila kuti iye wadali ochatila wa Yesu. 27 Nambho Banaba wadamutenga ni kumpeleka kwa atumwi. Iye wadaafotokozela atumwi umo Saulo wadakomanilana ni Ambuye mnjila ni umo Ambuye adakambilana ni iye. Banaba wadaakambilanjho umo Saulo wadalalikila mjhina la Yesu popande mandha kujha kumujhi wa Damasika. 28 Chimwecho Saulo wadakhala pamojhi ni atumwi ni kuyendela mu Yelusalemu yonjhe, niwalalikila kwa mbhavu ni popande mandha mjhina la Ambuye. 29 Ndiipo wadakambana ni kuchuchana ni Ayahudi yawo amakamba mkambo wa Chiyunani, nambho anyiiwo amafuna kumupha. 30 Yapo wokhulupilila adavela nghani zimenezo, adamtenga Saulo ni kupitanayo ku Kaisaliya, adamsiya kumeneko dala wapite ku Taliso.
31 Ndhawi imeneyo wandhu adamkhulupila Kilisito, adali ni mtendele mumujhi wa Yudea yonjhe, Galilaya ni Samaliya. Adathilidwa mtima ni Mzimu Woyela, adachuluka ni adakhala uku niamlambila Mnungu.
32 Yapo Petulo wamayendela malo yosiyanasiyana, wadapitanjho kwaayendela woyela yawo amakhala kumujhi wa Lida. 33 Kumeneko wadakomana ni mundhu mmojhi uyo watanidwa Eneya, uyo wadagona pachika kwa ndhawi ya vyaka nane ndande wadatopuwala. 34 Basi Petulo wadamkambila, "Eneya, Yesu wakulamicha. Uka ni uyale chika lako." Eneya wadauka pampajha. 35 Wandhu wonjhe amujhi wa ku Lida ni gombe la Shaloni yapo adamuona Eneya niwayenda, adaakhulupilila Ambuye.
36 Mmujhi wa Yopa mudali wamkazi mmojhi wokhulupilila uyo wamatanidwa Tabisa, pa Chiyunani Dokasi, mate yake, Ngolombwa. Wamkazi mmeneyo wamachita vabwino ni kwaathangatila wandhu wosauka siku zonjhe. 37 Ndhawi ijha iye wadadwala ni kumwalila. Thupi lake lidachukidwa ni kuliika kuchumba cha golofa. 38 Mujhi wa Yopa siudali patali ni mujhi wa Lida, wokhulupilila aku Yopa yapo adavela kuti Petulo wadali mumujhi wa Lida, adaatuma athenga awili kwa iye nikumpemba, niakamba, "Chonde ujhe kwathu sazino." 39 Chimwecho Petulo wadachoka, wadapita pamojhi ni athenga wajha. Yapo wadafika ku Yopa, wadapelekedwa golofa ku chumba chijha, uko wachikazi ambili yawo afedwa wachimuna adalizungulila thupi. Anyiiwo amalila ni kumlangiza Petulo malaya ni makhoti yayo wadakonja Dokasi yapo wadali wamoyo. 40 Petulo wadaatulucha wandhu wonjhe kubwalo yawo adali mchumba, wadagwada ni kupembhela. Ndiipo wadaling'anamukila lijha thupi ni kukamba, "Tabisa, uka!" Wamkazi yujha wadaphenula maso yake, ni yapo wadamuona Petulo, wadauka ni wadakhala. 41 Petulo wadamgwila jhanja ni kumuimicha. Ndiipo wadaatana wokhulupilila wonjhe mbaka wachikazi yawo afedwa wachimuna wao, ni kwaapacha wamkazi yujha wali wamoyo. 42 Nghani izi zidaveka kila malo ya Yopa, wandhu ambili adamkhulupilila Ambuye. 43 Petulo wadakhala ku Yopa kwa ndhawi yaitali pakhomo pa Simoni wokonja vikwetu.