Publicidade

Atos 12

Gulu la wandhu amkhulupilila Kilisito livutichidwa

1 Masiku yamweyajha mfumu Helode Agilipa wadaagwila ni kuyamba kwaavuticha wandhu akumojhi yawo adamkhulupilila Yesu. 2 Wadampha Yakobo mkuluwake wa Yohana kwa upanga. 3 Yapo wadaona yayo wachita yaakondwelecha Ayahudi, wadayendekela ni kumgwila Petulo. Ivi vidachitika ndhawi ya pwando la mabumunda yosathila amila. 4 Yapo wadamgwila Petulo wadamuika mndende, panjhi pa magulu yanayi ya alonda anayianayi kuti amlonde. Helode wamafuna kumuika Petulo pachogolo pa wandhu dala amlamule pa pwando la Pasaka likali losafike. 5 Chimwecho Petulo wadasungidwa mu ndende, nambho ndhawi imwewo, okhulupilila amampembhela kwa Mnungu popande kuleka.

Petulo watuluchidwa kubwalo kwa ndende

6 Usiku ujha likali losafike siku ilo Helode wadakamtulucha Petulo kubwalo, Petulo wadagona pakati pa alonda awili. Wadamangidwa maunyolo yawili, ni kudali alonda andhawi imeneyo nialonda khomo la ndende. 7 Mwachizulumukila mtumiki wa kumwamba wa Ambuye wadaima pa malo pajha, ni dangalila lidawala mndende mujha. Mtumiki yujha wadamnyukusa Petulo mndhiti ni kumuucha, niwakamba, "Choka chisangha!" Pamwepo maunyolo yajha yadamasuka ni kugwa panjhi. 8 Ndiipo mtumiki wa kumwamba wadakamba, "Manga lamba lako ni uvale malapasi yako." Petulo wadachita chimwecho. Ndiipo mtumiki yujha wadakamba, "Vala khoti lako unichate." 9 Petulo wadamchata mtumiki wa kumwamba kubwalo kwa ndende, popande kujhiwa kuti icho wamachita mtumiki wa kumwamba chidali cha uzene, wamaganiza kuti yadali masombhenya. 10 Adapita ulonda woyamba mbaka khomo lakawili la ndende, ni kufika pa khomo la chichulo ilo lipita ku mujhi. Khomo lidachekuka lene, ni anyiiwo adatuluka. Yapo adapita mkwakwa umojhi, yujha mtumiki wa kumwamba wa Mnungu wadamusiya Petulo mwachizulumukila.

11 Ndiipo Petulo wadajhiwa icho chidamchitikila, wadakamba, "Chipano najhiwa kuti ni vazene! Ambuye adamtuma mtumiki wa kumwamba wa Mnungu kujha kunichocha ku mbhavu za Helode Agilipa ni kunichocha mu yajha Ayahudi amalindilila yanichitikile."

12 Yapo wadajhiwa chimwecho, Petulo wadajha ku khomo kwa Maliya, amake a Yohana uyo wamatanidwanjho Maliko, uko wandhu ambili adakomana kuchita mapembhelo. 13 Petulo wadagogoda chicheko, ni mbowa uyo wamatanidwa Loda wadapita kumvechela. 14 Mwali mmeneyo yapo wadajhiwa kuti mvekelo umeneo udali wa Petulo, wadakondwa kwambili, ni wadabwelela popande kuchakula chicheko, ni kwaakambila wandhu kuti, "Petulo waima pakhomo!" 15 Anyiiwo adamkambila mwali yujha, "Iwe wobwabwazika eti!" Yapo wadayendekela kuchimikiza kuti ni Petulo, adakamba, "Lazima siwakhale mtumiki wa kumwamba wa Mnungu uwo wamthangatila iye."

16 Nambho Petulo wadayendekela kugogoda chicheko. Pothela adachekula chicheko, ni yapo adamuona Petulo, adazizwa. 17 Wadaalangiza chala kuti akhale chete, ni kuyamba kwaafotokozela umo Ambuye umo adamchochela mndende, niwakamba, "Mwaakambile Yakobo ni wandhu wina yawo adamkhulupilila Kilisito nghani izi." Ndiipo wadachoka ni kupita kumalo yanjake.

18 Umawa yapo udafika asikali wajha adali ni mandha yayakulu ndande ya yayo yachitika kwa Petulo. 19 Helode wadaalamula kuti amufunefune Petulo, nambho saadampheze. Ndiipo wadaafunjhichicha anyiwajha alonda ni kulamula kuti aphedwe.

Yapo yadapita yaya, Helode wadachoka ku Yudea ni kupita kukhala ku Kaisaliya kwa ndhawi.

Mfumu Helode Agilipa wamwalila

20 Helode wadakwiichidwa kupunda ni wandhu a ku Tilo ni Sidoni. Chimwecho wandhu adapita kukamuona iye mmagulumagulu. Adakambana ni Bulasito, mbowa wamkulu wa Holode uyo wadamkhulupilila, ni wadavomela kwaathangatila. Ndiipo Bulasito wadapita kwa Helode ni kupembha mtendele, pakuti jhiko lawo limapata chakudya kuchokela ku jhiko la mfumu Helode.

21 Basi yapo lidafika siku ilo adagwilizana kukomana, mfumu Helode Agilipa wadavala njhalu yachifumu ni kukhala pampando wachifumu, ni kuyamba kukamba ni wandhu. 22 Wandhu yawo adasonghana pajha adabula phokoso niakamba, "Uwu osati mvekelo wa mundhu, nambho ni mvekelo wa mnungu!" 23 Pamwepo mtumiki wa kumwamba wa Ambuye wadamgwecha Helode panjhi ndande siwadamtamande Mnungu. Wadagwilidwa ni utenda wa mwela ni kumwalila.

24 Nambho Mawu la Mnungu lidayendekela kuyenela ni kukula.

25 Banaba ni Saulo yapo adamaliza njhito ya Mnungu, adachoka ku Yelusalemu ali pamojhi ni Yohana uyo wamatanidwa Maliko.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-