Publicidade

Atos 11

Petulo wafotokoza umo watumidwila kwa wandhu osati Ayahudi

1 Atumwi ni okhulupilila wina a mu Yudea, adavela kuti wandhu osati Ayahudi nawo chinchijha adalandila mawu la Mnungu. 2 Ndiipo Petulo wadapita ku Yelusalemu, wajha Ayahudi adakhulupilila Yesu amafuna wandhu yawo osati Ayahudi achitidwe mdulidwe, adayamba kumtutumila iye niakamba, 3 "Iwe udapita mmakhomo mwa wandhu yawo sadachitidwe mdulidwe ni udadya pamojhi nawo!" 4 Chimwecho Petulo wadaafotokozela vindhu vonjhe ivo vidachitika nyumba kwa nyumba niwakamba,

5 "Siku limojhi yapo nidali mmapembhelo ku mujhi wa Yopa, nidaona masombhenya. Nidaona chindhu chachikulu ngati njhalu ya njhonga zinayi nichichika panjhi kuchokela kumwamba, ni kuima pafupi ni ine. 6 Nidapenyechecha mkati mwake, nidaona muli zinyama za miyendo inayi, zinyama za kuthengo, zinyama zokwawa ni mbalame. 7 Ndiipo nidavela mvekelo niyanikambila, ‘Petulo uka uphe ni udye!’ 8 Nambho ine nidakamba, ‘Notho Ambuye! Sinidadyepo chakudya chalichonjhe icho chakanizidwa kudyedwa kapina icho sichifunika mkamwa mwanga.’ 9 Mvekelo udavekanjho kuchokela kumwamba, ‘Vindhu ivo vavomelezedwa ni mnungu kudyedwa iwe sidavitana vindhu sivifunika.’ 10 Vindhu ivi vidachitika katatu, nimathelo yake vindhu vonjhe vidatengedwa kupita kumwamba. 11 Ndhawi imweijha wandhu atatu yawo adatumidwa kuchokela ku Kaisaliya adafika pa nyumba iyo nimakhala. 12 Mzimu woyela udanikambila nichogozane nawo popande kukhaikila. Nawo anyiwajha adamkhulupilila Yesu anjanga sita adachatana nane ku Kaisaliya ni kulowa mnyumba ya Konelio. 13 Wadatikambila umo mtumwi wa kumwamba wa Mnungu wadaimila pa nyumba yake ni kumkambila, ‘Atume wandhu ku Yopa akamtane mundhu uyo watanidwa Simoni Petulo. 14 Iye siwakukambile mawu yayo siyakuombole iwe pamojhi ni nyumba yako yonjhe.’ 15 Yapo nidayamba kukamba, Mzimu Woyela udaachikila ngati umo udachitila kwa ife poyamba. 16 Ndiipo nidakumbukila yajha adakamba Ambuye, ‘Yohana wadabatiza kwa majhi, nambho anyiimwe simubatizidwe kwa Mzimu Woyela.’ 17 Ijhiwika kuti Mnungu wadaapacha wandhu osati Ayahudi utumiki wofanana ni uwo tidapachidwa ife yapo tidaakhulupilila Ambuye Yesu Kilisito, ine nidali yani kuti nimchuche Mnungu?"

18 Yapo adavela chimwechi, adasiya kwaachucha ni kuyamba kumkweza Mnungu, niakamba, "Mnungu waapacha wandhu osati Ayahudi malo yolapa kuti apate umoyo wamuyaya."

Wandhu adamkhulupila Kilisito ku Antiokia

19 Wokhulupilila wina yawo adamwazika ndande ya mavuto yayo yadachitika yapo wadaphedwa Sitifano, adapita kutali mbaka ku Fonesiya, Kipulo ni ku Atioki, nauzila uthenga wa Mnungu kwa Ayahudipe. 20 Nambho wokhulupilila anjake yawo adachokela ku Kipulo ni Kilene, adapita ku Antiokia ni kukambilana ni wandhu osati Ayahudi, niwaakambila uthenga wabwino wa nghani za Ambuye Yesu. 21 Ambuye wadachogoza kwa mbhavu yake, ni gulu la wandhu ambili lidakhulupilila ni kumng'anamukila Ambuye.

22 Nghani za wandhu wajha zidafika mbaka kwa wandhu adamkhulupilila Yesu a ku Yelusalemu, chimwecho adamtuma Banaba wapite ku Antiokia. 23 Yapo wadafika kumeneko ni kuona umo Mnungu wadaapachila mwawi wandhu, wadakondwa kupunda ni wadaapembha ayendekele kukhala okhulupilika kwa Ambuye. 24 Banaba wadali mundhu wabwino, wachogozedwa ni mbhavu za Mzimu Woyela ni chikhulupililo, ndande ya Banaba wandhu ambili amachuluka kwa Ambuye.

25 Ndiipo Banaba wadapita ku mujhi wa Taliso kukamfunafuna Saulo. 26 Yapo wadampheza, wadapitanayo ku Antiokia. Wonjhe awili adakhala ni gulu ilo lidamkhulupilila Kilisito kwa chaka cha mbhumbhu, uku niayaluza gulu lalikulu la wandhu. Kumeneko ku Antiokia nde kwa mala yoyamba wandhu adayamba kutanidwa Akilisito.

27 Ndhawi imweyo alosi wina adachoka ku Yelusalemu adajha ku mujhi wa Antiokia. 28 Basi Mundhu mmojhi uyo watanidwa Agabasi, wadaima ni kulosa kwa mbhavu za Mzimu Woyela kuti njala yaikulu siijhe pa jhiko lonjhe lapanjhi. Njala imeneyo idajha ndhawi ya ulamulilo wa mfumu Tibelio. 29 Wajha ochatila kila mmojhi wadachocha mthandizo kwa okhulupilila anjao yawo amakhala ku Yudea ngati umo adakhozela. 30 Nikwaatuma Banaba na Sauli apeleke njhembe kwa waakulu agulu la wandhu yawo amkhulupilila Kilisito.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-19_11-20-24-