Publicidade

Atos 23

1 Poolo wadaapenyechecha athenga a bwalo la achogoleli ni kukamba, "Achabale wanga Ayahudi, namtumikila Mnungu kwa mtima woyela mbaka lelo lino." 2 Mjhukulu wamkulu Ananiya wadaalamula anyiwajha adaima pafupi ni iye kuti ambule khofi. 3 Ndiipo Poolo wadamkambila Ananiya, "Mnungu siwakubule khofi nawenjho mgunghuli! Iwe uli ngati phupa ilo lanyekedwa langi yoyela. Pakuti wakhala pamenepo kwaalamula wandhu kuti unilamule ine kupitila thauko, nambho iwe uliwananga thauko pa kwaakambila anyiiwo kuti anibule ine!"

4 Wandhu wajha adaima pafupi ni Poolo adamkambila, "Ndande yanjhi, umtukwana Mjhukulu Wamkulu wa Mnungu!"

5 Poolo wadaayangha, "Achaabale wanga Ayahudi, sinidajhiwe kuti iye wadali Mjhukulu Wamkulu. Pakuti yalembedwa, ‘Usadamkambila mawu yoipa mchogoleli wa wandhu wako.’ "

6 Poolo yapo wadajhiwa kuti wandhu wina mgulu mujha adali Asadukayo ni wina adali Afalisayo, wadakweza mvekelo wake niwakamba, "Abale wanga aku ayahudi! Ine ni Mfalisayo, mwana wa Mfalisayo. Napelekedwa pa bwalo la milandu ndande nikhulupilila kuti wandhu yawo amwalila siahyuke!"

7 Poolo yapo wadakamba chimwecho, padachokela mchuchano pakati pa Afalisayo ni Asadukayo, ni gulu lidagawika kukhala mabendeka yawili. 8 Adagawanyika ndande Asadukayo amakhulupilila kuti wandhu amwalila saahyuka ni kuti kulibe atumiki akumwamba a Mnungu kapina mizimu woyela, nambho Afalisayo akhulupilila vonjhe vitatu vilipo. 9 Phokoso lidapunda kukula, ni akumojhi a oyaluza a Thauko yawo adali agulu la Afalisayo adaima ni kuchuchana kwa mbhavu niakamba, "Sitiona chilichonjhe icho walakwa mundhu uyu! Ikhozeka atumiki akumwamba a Mnungu kapina mzimu woyela wakambana naye!"

10 Mchuchano udapunda kukhala waukulu mbaka wamkulu wa asikali wadaopa kuti Poolo siwadulidwe vipinjilivipinjili. Chimwecho wadaalamula asikali wake kulowelela lijha gulu, kuti amchoche Poolo ni kumbweza mkati mwa nyumba ya asikali.

11 Usiku uwo udachata Ambuye adaima pafupi ni Poolo ni kukambila, "Usadaopa! Ngati umo udakambila nghani zanga muno mu Yelusalemu, ni ufunikanjho ukaakambile wandhu nghani zanga kujha ku Loma."

Ayahudi afuna njhila ya kumpha Poolo

12 Yapo kudacha Ayahudi adachita adapita pambhepete kuchita msonghano. Adaahidi kuti siadya kapina kumwa chindhu chilichonjhe mbaka yapo siamuphe Poolo. 13 Wandhu yawo adakambilana yameneyo adali wandhu wopitilila alobaini. 14 Ndiipo adapita kwa mjhukulu wamkulu ni achogoleli wa azee ni kukamba, "Ive talumbila kuti sitidya kapina kumwa mbaka yapo sitimuphe Poolo. 15 Chipano anyiimwe pamojhi ni achogoleli a bwalo la milandhu, mpelekeleni uthenga wamkulu wa asikali kuti wakupelekeleni Poolo, uku ni mjhichita kuti mfuna kujhiwa icho walakwa. Niife sitimpe yapo siwamajhe."

16 Nambho mwana wa mlongo wake Poolo wadavela ugunghuli wao wa kufuna kumpha Poolo, chimwecho wadapita ku nyumba ya asikali ni kumkambila Poolo. 17 Ndiipo Poolo wadamtana wamkulu wa gulu la asikali ni kumkambila, "Mpeleke mnyamata uyu kwa mchogoleli wa asikali, wali ni chindhu icho wafuna kumkambila." 18 Ndipo yujha wamkulu wa gulu la Asikali wadamtenga mnyamata yujha ni kupita nayo kwa wamkulu wa asikali niwakamba, "Poolo yujha womangidwa wadanitana ni kunipembha kuti nimpeleke mnyamata uyu kwanu, ndande wali ni chindhu icho wafuna kukukambilani."

19 Yujha wamkulu wa asikali wadamgwila jhanja yujha mnyamata ni kupita nayo ku mbhepete ni kumfunjha, "Ufuna kunikambila chiyani?"

20 Mnyamata yujha wadakamba, "Ayahudi agwilizana kuti mawa sakupembheni kuti muumpeleke Poolo ku bwalo lalikulu, niajhichita kuti afuna kujhiwa bwino volakwa vake. 21 Nambho usadavomela, pakuti kuli wandhu ambili kupitilila alobaini yawo sambisalile. Alumbila osadye kapina kumwa mbaka yapo saamuphe Poolo. Anyiiwo akonjeka kuchita chimwecho ni alindilila lamulo lanupe."

22 Wamkulu wa asikali wadamkambila yujha mnyamata, "Usamkambila mundhu waliyonjhe kuti wanikambila nghani izi, nayo wadamsiya wajhipita."

Poolo wasamuchilidwa ku Kaisaliya

23 Ndiipo yujha wamkulu wa asikali wadaatana wakulu a magulu yawili ya asikali ni kwakambila, "Akonjekele asikali mia mbili, ni okwela falasi sabini ni asikali ali ni misongha miya mbili akhale tayali kupita ku Kaisaliya saa tatu lelo lino usiku. 24 Mkonjekelenjho falasi wina yawo siwakwele Poolo, mumfikize bwino kwa mlamuli Felikisi wa kujhiko la Yudea." 25 Ndiipo yujha wamkilu wa asikali wadalembela kalata Felikisi iyo idakamba kuti,

26 "Ine Kilaudio Lisia, nikulembela iwe mlamuli Felikisi, ndande ya kukulonjela. 27 Ayahudi adamgwila mundhu huyu ni kufuna kumpha, nambho yapo nidapata uthenga kuti iye ni mundhu wa kujhiko la Loma nidajha ni magulu yanga ya asikali nidamuombola. 28 Nimafuna kujhiwa wali ni mlandu wanji, chimwecho nidapitanayo pachopgolo pa bwalo lawo lalikulu la milandu. 29 Nidajhiwa kuti siwadachite chilichonjhe icho chimchita waphedwe kapina kuikidwa mndende, nambho adampacha mlandu wa machuchano ya Thauko lawo achinawene. 30 Yapo nidakambidwa kuti Ayahudi ali mpango wa kufuna kumupha mundhu uyu. Nalamula kuti nimpeleke kwako. Naatuma Ayahudi yawo ampacha mlandu kuti akukambile icho walakwa."

31 Chimwecho asikali adachata lamulo ilo adapachidwa, adamtenga Poolo ndhawi ya usiku ni kumpeleka mbaka ku Antipatili. 32 Siku lakawili asikali ayenda pamwendo adabwela kunyumba ya asikali, wadaasiya anyiwajha adakwela falasi ayendekele ni ulendo wa kumpeleka poolo. 33 Anyiiwo adamtenga ni kupita nayo ku Kaisaliya ni kumpelekela Felikisi wamkulu wa wamkulu wa mujhi ni adampacha ijha kalata, ni adamuika Poolo panjhi pa ulonda wake. 34 Mlamuli Felikisi yapo wadaisoma kalata ijha, wadamfunjha Poolo kuti wadachokela mumujhi uti. Yapo wadavela kuti wachokela mumujhi wa Kilikiya, 35 wadakamba, "Sinivechele mlandu wako akathofika yawo akupacha mlandu." Ndiipo wadapeleka lamulo kuti wasungidwe bwino mu nyumba ya chifumu ya Helode.

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-18_14-04-22-