1 Chipano, kuchokana ni zijha nghani mdalemba.
Anyiimwe mdafunjha kuti ni mbasa wammuna siwadakwata. 2 Nambho chimo la chigololo ni loyipa, chimwecho kila wammuna wakhale ni wamkazi wake, ni kila wamkazi wakhale ni wammuna wake. 3 Wammuna wachite umo ifunikila kwa mkazake, ni wamkazi wachite umo ifunikila kwa mmunake, ni kila mmojhi wamkwaniliche mnjake icho chifunika. 4 Wamkazi walibe lamulo pamwamba pa thupi lake, nambho mmunake wali nilamulo pamwamba pa thupi la mkazake, chinchijha wammuna nayonjho walibe lamulo pamwamba pathupi lake, nambho mkazake wali nilamulo pa mwamba pathupi la mmunake. 5 Msadamanana nambho ikakhala mwavomelezana dala mpheze ndhawi ya mapembhelo, ndiipo mbwelelenjho ili Mdani wa Mnungu siwadapheza kukuikani mmayeso ndande ya kulepela kuchekeleza mafuno yanu.
6 Nikamba yaya kukupachani maganizo osati lamulo. 7 Ila nikonda wandhu onjhe akhale ngati ine umo nili, nambho kila mmojhi wali ni mbhaso yake kuchoka kwa Mnungu, mundhu mmojhi mbhaso iyi, ni mwina mbhaso ijha.
8 Chipano nikukambilani anyiimwe simuda kwate, nimwafedwa ni achamunanu, mbasa muendekele kukhala popande kukwata ni kukwatiwa ngati umo nili ine. 9 Nambho ngati simukhoza kuchekeleza makhumbilo yanu, chimwecho mkwate kapina kukwatiwa, pakuti mbasa kukwata kapina kukwatiwa kusiyana nikuhla ni kukhumbila.
10 Nambho kwa anyiwajha akwata nili ni lamulo. Wamkazi siwadasiyana ni mmunake, 11 nambho ikakhala wamkazi wasiyana nimmunake, siwada kwatiwa, kapina wabwelelane ni mmunake, ni wammuna siwadalemba kalata ya kumsiya mkazake.
12 Nambho kwa wina, ine nikukambilani osati Ambuye akamba, ngati wammuna wali ni wamkazi, siwada khulupilile, ni wamkazi wavomela kukhala nayo siwadamsiya. 13 Wamkazi uyo wamkhulupilila Kilisito, ngati wali ni wammuna uyo siwadakhulupilile, niwammuna mmeneyo wavomela kukhala nayo siwadamsiya. 14 Kwa wammuna siwadakhulupile walandilidwa kwa Mnungu kwa kulunjana ni mkazake, ni wamkazi siwada khulupilile walandilidwa ni Mnungu kwa kulunjana ni wammuna wamkhulupilila Kilisito. Ngati siidakali chimwecho wana wanu sadakavomelezedwa ni Mnungu, kumbe chipano avomelezedwa kukhala wana a Mnungu. 15 Nambho, wammuna kapina wamkazi siwadakhulupile wafuna kumsiya mnjake uyo wakhulupilila, chimwecho wachite chimwecho. Pakuchita chimwecho, wamkazi kapina wammuna wakhulupila siwamangika ndande Mnungu watitana tikhale ni umoyo wa mtendele. 16 Iwe wamkazi wamkhulupilila Yesu ujhiwa bwanji, ngati siumuombola mmunako? Kapina iwe wammuna ujhiwa bwanji ngati siumuombola mkazako?
17 Nambho kila mmojhi wajhikhala ngati umo walamulidwa ni Ambuye, ngati umo watanidwila ni Mnungu. Ili ni lamulo ilo niyaluza mu magulu yonjhe ya yao amkhulupilila Yesu. 18 Ngati, mundhu wadatanidwa wathochitidwa mdulidwe, wasadajhichita kuti siwadadulidwe, ni ngati yapo wadatanidwa siwadadulidwe basi siwadadulidwa. 19 Kuchitidwa mdulidwe osati kandhu, nikukhala osachitidwe mdulidwe osati kandhu, nambho kuvela nikuyachata malamulo ya Mnungu. 20 Kila mmojhi wajhikhala ngati mujha Mnungu wadamtana. 21 Bwanji udatanidwa uli kapolo? Usadaona kuipa, ngati ukaona ufulu tumila malo ulinayo chipano, kusiyana ni nyengo ina yaliyonjhe. 22 Kwa kapolo watanidwa ni Ambuye iye wakhala mundhu wa ufulu, chimwecho watanidwa wali mundhu wa ufulu iye wakhala kapolo wa Kilisito. 23 Mnungu wakughulani kwa mtengo waukulu, kuti msadakhala kapolo a wandhu. 24 Abale wanga kilammojhi wakhale ni pachogolo pa Mnungu ngati mujha wadali yapo wadatanidwa.
25 Chipano kuchokana ni yajha mwalemba ya wandhu siadakwatiwe, nilibe lamulo kuchokela kwa Ambuye, nambho ine nichocha ganizo ine uyo kwa lisungu la Ambuye nifuni kuaminidwa. 26 Kuchokana ni vuto ilo lilipo chipano, niona mbasa mkhale ngati umo muli. 27 Bwanji wakwata? Chimwecho usada funa kusiyana ni mkazako. Bwanji siudakwate? Usada funa wamkazi. 28 Nambho ngati siukwate, siuchita machimo, ningati wamkazi siwada kwatiwe waka kwatiwa siwachita machimo. Nambho anyiyao akwatana siapheze masauko mu umoyo uwu, nane nifuna simuda pitila masauko yameneyo.
29 Abale wanga mateyake ndhawi ya khalila ni yochepa, kuyamba sazino anyiyao akwata akhale ngati siadakwate, 30 anyiyao ali mzaya, akhale ngati anyiyao siali mzaya, nianyiyao akondwela akhale ngati sakondwela, nianyiyao agula akhale ngati alibe cho ghula, 31 Wajha ajhichaucha ni vindhu va jhiko lino, akhale ngati alibenavo njhito. Pakuti pa jhiko lino silikhalila ndhawi yambili.
32 Nidakakonda anyiimwe msamakhaikila. Mundhu uyo walibe wamkazi wapota njhito ya Ambuye, ni ndande wafuna kumkondwelecha Ambuye. 33 Nambho wammuna uyo wakwata wapota njhito pavindhu va jhiko dala wamkondweleche mkazake, 34 ni waguzidwa kawili. Wammkazi siwada kwatiwe wajhi vuticha ni vindhu va Ambuye, nambho wammkazi wakwatiwa wajhichaucha ni vindhu va jhiko lino kuti wamkondweleche mmunake.
35 Nikamba yaya ndande nifuna kukutangatilani. Nifuna mkhale ni mpango uwo ufunika kuti mkhoze kwatumikila Ambuye bwino.
36 Mundhu waliyonjhe wakaona siwamchitila mwali wake ivo wakondwela, niika khala wakula, niwakafuna kukwatiwa basi wachite umo wafunila, siwachita machimo wamkwatepe. 37 Nambho ngati wammuna, wakalamula mwenewake mumtima mwake osakwate popande kukakamizidwa ni walionjhe, ningati wakhoza kujhilamula basi wachita bwino siwadamkwata wamkaziyo. 38 Chimwecho wammuna uyo wakwata wachita bwino, ni wammuna uyo siwakwata wachita bwino kupunda.
39 Wammkazi wakwatiwa wamangidwa ni thauko ngati pe wammuna wali wamoyo, nambho ngati wammuna wamwalila basi wamkazi mmeneyo wakakonda wakhoza kukwatiwa ni wammuna mwina, nambhope wakwatiwe ni wammuna uyo wamkhulupilila Yesu. 40 Umo nionela ine mbasa wakhale chimwecho popande kukwatiwa, yameneyo ni maganizo yanga, ni nikhulupilila kuti nilinawo Mzimu wa Mnungu.