Fanizo la Mwana Wolowerera
11 Yesu anapitiriza kunena kuti, "Panali munthu amene anali ndi ana aamuna awiri. 12 Wamngʼonoyo anati kwa abambo ake, ‘Abambo, patseni gawo langa la chuma chanu.’ Ndipo iye anawagawira awiriwo chuma chawo.
13 "Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko. 14 Iye atawononga zonse, kunagwa njala yoopsa mʼdziko lonselo ndipo anayamba kusauka. 15 Iye anapita kwa nzika ina ya dzikolo nakakhala naye ndi kumagwira ntchito, amene anamutumiza ku munda kukadyetsa nkhumba. 16 Iye analakalaka atakhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumbazo zinkadya, koma panalibe wina amene anamupatsa kanthu.
17 "Maganizo ake atabweramo, iye anati, ‘Ndi antchito angati a abambo anga amene ali ndi chakudya chimene amadya nʼkutsalako ndipo ine ndili pano kufa ndi njala! 18 Ine ndinyamuka ndi kubwerera kwa abambo anga ndipo ndikati kwa iwo: abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi kwa inu. 19 Ndine wosayeneranso kutchedwa mwana wanu; munditenge ngati mmodzi wa antchito anu.’ 20 Ndipo iye ananyamuka ndi kupita kwa abambo ake.
"Koma iye akanali patali, abambo ake anamuona ndipo anamvera chisoni; anathamangira mwanayo, namukumbatira ndi kupsompsona.
21 "Mwanayo anati, ‘Abambo, ine ndachimwira kumwamba ndi inunso. Ine sindiyenera konse kutchedwa mwana wanu.’
22 "Koma abambowo anati kwa antchito ake, ‘Fulumirani! Bweretsani mkanjo wabwino kwambiri ndipo mumuveke. Muvekeni mphete ndi nsapato. 23 Bweretsani mwana wangʼombe wonenepa ndipo iphani. Tiyeni tikhale ndi phwando ndi kukondwerera. 24 Pakuti mwana wangayu anali wakufa, ndipo ali ndi moyonso; iye anatayika ndipo wapezeka.’ Chomwecho anayamba kukondwerera.