Za Munthu Wachuma ndi Lazaro
19 "Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. 20 Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse 21 ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.
22 "Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. 23 Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. 24 Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’
25 "Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. 26 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’
27 "Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, 28 pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’
29 "Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’
30 "Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’
31 "Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ "