12 Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali 13 ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, "Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!"
14 Iye atawaona, anati, "Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe." Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.
15 Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. 16 Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.
17 Yesu anafunsa kuti, "Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? 18 Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?" 19 Pamenepo anati kwa iye, "Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe."