Publicidade

Lucas 18

Fanizo la Mayi Wakhama pa Kupempha

1 Kenaka Yesu anawuza ophunzira ake fanizo kuwaonetsa kuti iwo ayenera kumapemphera nthawi zonse ndikuti asafowoke. 2 Iye anati, "Mʼmudzi wina munali woweruza wosaopa Mulungu ngakhalenso kulabadira za anthu. 3 Ndipo panali mkazi wamasiye mʼmudzimo amene ankabwerabwera kwa iye ndi dandawulo lake kuti, Mundiweruze mlandu mwachilungamo pakati pa ine ndi otsutsana nane.

4 "Kwa nthawi yayitali woweruzayo ankakana. Koma pa mapeto analingalira nati, Ngakhale kuti sindiopa Mulungu kapena kulabadira za anthu, 5 koma chifukwa chakuti mkazi wamasiyeyu akundivutitsa, ine ndimuweruzira mlandu wake mwachilungamo kuti asanditopetse ndi kubwerabwera kwakeko!’ "

6 Ndipo Ambuye anati, "Tamvani zimene woweruza wopanda chilungamoyu wanena. 7 Tsono chingamuletse nʼchiyani Mulungu kubweretsa chilungamo kwa osankhika ake, amene amalira kwa Iye usana ndi usiku? Kodi adzapitirirabe osawalabadira? 8 Ine ndikukuwuzani inu, adzaonetsetsa kuti alandire chilungamo, ndiponso mofulumira. Komabe, pamene Mwana wa Munthu akubwera, kodi adzapeza chikhulupiriro pa dziko lapansi?"

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-29_22-07-56-