Pular para o conteúdo
Publicidade

LUKA 19

Zakeyu Apulumutsidwa

1 Yesu analowa mu Yeriko napitirira. 2 Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. 3 Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. 4 Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.

5 Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, "Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero." 6 Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.

7 Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, "Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa."

8 Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, "Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi."

9 Yesu anati kwa iye, "Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10 Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também