Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero
28 Yesu atatha kunena izi, anayendabe kupita ku Yerusalemu. 29 Iye atayandikira ku Betifage ndi Betaniya pa phiri lotchedwa Olivi, Iye anatuma awiri a ophunzira nati kwa iwo, 30 "Pitani mʼmudzi uli patsogolo panu, mukakalowa mʼmudzimo, mukapeza mwana wabulu womangiriridwa amene wina aliyense sanakwerepo. Mukamumasule ndi kubwera naye kuno. 31 Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumumasula mwana buluyo?’ Mukamuwuze kuti, ‘Ambuye akumufuna.’ "
32 Otumidwawo anapita nakamupeza mwana wabulu monga momwe Yesu anawawuzira. 33 Pamene ankamasula mwana wabuluyo, eni ake anawafunsa kuti, "Nʼchifukwa chiyani mukumasula mwana wabuluyo?"
34 Iwo anayankha kuti, "Ambuye akumufuna."
35 Iwo anabweretsa buluyo kwa Yesu, naponya zovala zawo pa bulupo ndi kumukwezapo Yesu. 36 Pamene ankapita, anthu anayala zovala zawo mu msewu.
37 Iye atafika pafupi ndi pamene msewu umatsikira ku phiri la Olivi, gulu lonse la ophunzira linayamba kuyamika Mulungu mwachimwemwe ndi mawu ofuwula chifukwa cha zodabwitsa zonse anaziona.
38 "Yodala mfumu imene ikubwera mʼdzina la Ambuye!"
"Mtendere kumwamba ndi ulemerero mmwambamwamba!"
39 Ena mwa Afarisi mʼgulumo anati kwa Yesu, "Aphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anu!"
40 Iye anayankha kuti, "Ine ndikukuwuzani kuti, ngati atakhala chete, miyala idzafuwula."