Pular para o conteúdo
Publicidade

LUKA 2

22 Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. 23 (Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, "Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa"), 24 ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: "Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri."

25 Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26 Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye. 27 Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, 28 Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:

29 "Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza,

tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere.

30 Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,

31 chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse,

32 kuwala kowunikira anthu a mitundu ina

ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli."

33 Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye. 34 Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: "Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, 35 kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso."

36 Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa, 37 ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. 38 Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.

Veja também