Yesu mʼNyumba ya Mulungu
41 Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. 42 Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. 43 Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. 44 Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. 45 Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. 46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47 Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, "Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe."
49 Iye anawafunsa kuti, "Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?" 50 Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.
51 Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.
52 Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.