19 Ndipo Iye anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema, nagawira iwo nati, "Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine."
20 Chimodzimodzinso, utatha mgonero, anatenga chikho nati, "Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga, amene akhetsedwa chifukwa cha inu.