Petro Akana Yesu
54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, "Munthu uyu anali ndi Yesu."
57 Koma Petro anakana nati, "Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu."
58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, "Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo."
Petro anayankha kuti, "Munthu iwe, ayi sindine."
59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, "Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya."
60 Petro anayankha kuti, "Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa." Pamene iye ankayankhula, tambala analira. 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, "Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu." 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.