33 Pamene anafika pamalo otchedwa Bade, anamupachika Iye pamodzi ndi achifwambawo, mmodzi kudzanja lake lamanja ndi winayo la ku lamazere. 34 Yesu anati, "Atate, akhululukireni, pakuti sakudziwa chimene akuchita." Ndipo anagawana malaya ake mochita maere.
35 Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, "Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo."
36 Asilikalinso anabwera ndi kumunyoza Iye. Iwo anamupatsa vinyo wosasa, 37 ndipo anati, "Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha."
38 Ndipo panalembedwa chikwangwani pamwamba pake chimene chinati: uyu ndi mfumu ya ayuda.
39 Mmodzi wa achifwambawo, amene anapachikidwa, anamunenera Iye zamwano nati, "Kodi sindiwe Khristu? Dzipulumutse wekha ndi ifenso!"
40 Koma wachifwamba winayo anamudzudzula iye nati, "Suopa Mulungu, iwenso ukulandira chilango chomwechi? 41 Ife tikulangidwa mwachilungamo, pakuti ife tikulandira monga mwa ntchito zathu. Koma munthu uyu sanachimwe kanthu."
42 Kenaka anati, "Yesu, mundikumbukire ine pamene mulowa mu ufumu wanu."
43 Yesu anayankha kuti, "Zoonadi, ndikukuwuza kuti lero lino udzakhala ndi Ine mʼparadaiso."