Zochitika pa Njira ya ku Emau
13 Ndipo tsiku lomwelo, awiri a iwo ankapita ku mudzi wotchedwa Emau, pafupifupi makilomita khumi ndi imodzi kuchokera ku Yerusalemu. 14 Iwo ankayankhulana za zonse zimene zinachitikazo. 15 Pamenepo Yesu mwini wake anabwera ndi kuyenda nawo pamodzi; 16 koma iwo sanamuzindikire.
17 Iye anawafunsa kuti, "Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?"
Iwo anayima ndi nkhope zakugwa. 18 Mmodzi wa iwo wotchedwa Kaliyopa anamufunsa kuti, "Kodi ndiwe wekha wokhala mu Yerusalemu amene sukudziwa zinthu zimene zachitika mʼmasiku awa?"
19 Iye anafunsa kuti, "Zinthu zotani?"
Iwo anayankha nati, "Za Yesu wa ku Nazareti, Iye anali mneneri, wamphamvu mʼmawu ndi mu zochita pamaso pa Mulungu ndi anthu onse. 20 Akulu a ansembe ndi oweruza anamupereka Iye kuti aphedwe, ndipo anamupachika Iye; 21 koma ife tinkayembekezera kuti Iye ndiye amene akanawombola Israeli. Ndipo kuwonjeza apo, lero ndi tsiku lachitatu chichitikireni izi. 22 Kuwonjezanso apo, ena mwa amayi athu atidabwitsa ife. Iwo anapita ku manda mmamawa 23 koma sanakapeze mtembo wake. Iwo anabwera ndi kudzatiwuza ife kuti anaona masomphenya a angelo amene anati Yesu ali moyo. 24 Kenaka ena mwa anzathu anapita ku manda ndipo anakapeza monga momwe amayiwo ananenera, koma Iye sanamuone."
25 Iye anawawuza kuti, "Inu ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zimene aneneri ananena! 26 Kodi Khristu sanayenera kumva zowawa izi ndipo kenaka ndi kulowa mu ulemerero wake?" 27 Ndipo kuyambira ndi Mose ndi aneneri onse Iye anawafotokozera zimene zinalembedwa mʼmalemba wonse zokhudzana ndi Iye mwini.
28 Atayandikira mudzi omwe amapitako, Yesu anachita ngati akupitirira. 29 Koma iwo anamupempha Iye kwambiri kuti, "Mukhale ndi ife, popeza kwatsala pangʼono kuda, ndipo dzuwa lili pafupi kulowa." Ndipo Iye anapita kukakhala nawo.
30 Iye ali pa tebulo pamodzi nawo, anatenga buledi ndipo anayamika, nanyema nayamba kuwagawira. 31 Kenaka maso awo anatsekuka ndipo anamuzindikira Iye, ndipo anachoka pakati pawo. 32 Iwo anafunsana wina ndi mnzake kuti, "Kodi mitima yathu sinali kutentha mʼkati mwathu pamene Iye ankayankhulana nafe pa njira ndi mmene anatitsekulira malemba?"
33 Nthawi yomweyo iwo anayimirira ndi kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapeza khumi ndi mmodziwo ndi ena anali nawo nasonkhana pamodzi 34 ndipo anati, "Ndi zoonadi! Ambuye auka ndipo anaonekera kwa Simoni." 35 Kenaka awiriwo anawawuza zimene zinachitika pa njira, ndi mmene iwo anamudziwira Yesu, Iye atanyema buledi.