Ubatizo wa Yesu
21 Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. 22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: "Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe."