18 "Mzimu wa Ambuye ali pa Ine;
chifukwa wandidzoza
kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka.
Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe
ndi kwa osaona kuti apenyenso,
kumasulidwa kwa osautsidwa,
19 ndi kulalikira za nthawi imene Ambuye adzakomere mtima anthu awo."