Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba
1 Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. 2 Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. 3 Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.
4 Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, "Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba."
5 Simoni anayankha kuti, "Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka."
6 Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. 7 Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.
8 Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, "Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!" 9 Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, 10 chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo.
Kenaka Yesu anati kwa Simoni, "Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu." 11 Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.