Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 5

18 Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. 19 Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.

20 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, "Mnzanga, machimo ako akhululukidwa."

21 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, "Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?"

22 Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, "Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu? 23 Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, Machimo ako akhululukidwa,kapena kunena kuti, Nyamuka ndipo yenda? " 24 Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, "Ine ndikuwuza iwe kuti, Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ " 25 Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu.

Veja também