Pular para o conteúdo
Publicidade

LUKA 6

6 La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala. 7 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata. 8 Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, "Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa." Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo.

9 Kenaka Yesu anawawuza kuti, "Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?"

10 Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, "Wongola dzanja lako." Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também