Yesu Aukitsa Mwana wa Mayi Wamasiye
11 Zitangotha izi, Yesu anapita ku mudzi wa Naini ndipo ophunzira ake ndi gulu lalikulu la anthu linapita naye pamodzi. 12 Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye. 13 Ambuye atamuona mayiyo, mtima wawo unagwidwa naye chifundo ndipo anati, "Usalire."
14 Kenaka anapita nakakhudza chithatha cha maliro ndipo amene anachinyamulawo anayima. Iye anati, "Mnyamata, ndikukuwuza kuti, dzuka!" 15 Wakufayo anakhala tsonga ndi kuyamba kuyankhula, ndipo Yesu anamupereka mnyamatayo kwa amayi ake.
16 Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, "Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake." 17 Mbiriyi inafalikira ku Yudeya konse ndi ku madera ozungulira.