31 "Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? 32 Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,
" ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,
koma inu simunavine.
Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,
koma inu simunalire.’
33 Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ 35 Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse."
Yesu Adzozedwa ndi Mayi Wochimwa
36 Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo. 37 Mayi amene amakhala moyo wauchimo mu mzindawo atadziwa kuti Yesu akudya ku nyumba ya Mfarisiyo, anabweretsa botolo la mafuta onunkhira a alabasta.