Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 8

Yesu Aletsa Namondwe

22 Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, "Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja." Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka. 23 Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.

24 Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, "Ambuye, Ambuye, ife tikumira!"

Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata. 25 Iye anafunsa ophunzira ake kuti, "Chikhulupiriro chanu chili kuti?"

Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, "Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye."

Veja também