Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu
40 Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera. 41 Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake, 42 chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa.
Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza. 43 Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa. 44 Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.
45 Yesu anafunsa kuti, "Wandikhudza ndani?"
Onse atakana, Petro anati, "Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani."
46 Koma Yesu anati, "Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine."
47 Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo. 48 Kenaka anati kwa iye, "Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere."
49 Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, "Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa."
50 Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, "Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa."
51 Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo. 52 Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, "Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo."
53 Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira. 54 Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, "Mwana wanga, dzuka!" 55 Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya. 56 Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.