Yesu Atuma Ophunzira ake Khumi ndi Awiri
1 Yesu atawayitana khumi ndi awiriwo pamodzi, Iye anawapatsa mphamvu ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda zonse ndi kuchiritsa matenda. 2 Ndipo Iye anawatumiza kukalalikira za ufumu wa Mulungu ndi kukachiritsa odwala. 3 Iye anawawuza kuti, "Musatenge kanthu paulendo. Musatenge ndodo, thumba, buledi, ndalama, ndi malaya apadera. 4 Nyumba iliyonse imene mulowa, mukhale momwemo kufikira mutachoka mu mzindawo. 5 Ngati anthu sakulandirani, sasani fumbi la kumapazi anu pomwe mukuchoka mu mzinda wawo ngati umboni owatsutsa." 6 Ndipo iwo ananyamuka napita, mudzi ndi mudzi, kulalikira Uthenga Wabwino ndi kuchiritsa anthu paliponse.