Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 9

12 Chakumadzulo dzuwa litapita, khumi ndi awiriwo anabwera kwa Iye ndipo anati, "Uzani gulu la anthuli lichoke kuti apite ku midzi yotizungulira ndi madera a ku mudzi kuti akapeze chakudya ndi pogona, chifukwa kuno ndi kuthengo."

13 Iye anayankha kuti, "Apatseni chakudya kuti adye."

Iwo anayankha kuti, "Ife tili ndi malofu a buledi asanu okha ndi nsomba ziwiri, pokhapokha titapita kukagula chakudya cha gulu la anthu onsewa." 14 (Pamenepo panali amuna pafupifupi 5,000).

Koma Iye anati kwa ophunzira ake, "Akhazikeni pansi mʼmagulu a anthu pafupifupi makumi asanu." 15 Ophunzira ake anachita zomwezo ndipo aliyense anakhala pansi. 16 Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri zija anayangʼana kumwamba, nayamika ndipo anazigawa. Kenaka anazipereka kwa ophunzira ake kuti azipereke kwa anthu. 17 Onse anadya nakhuta, ndipo ophunzira ake anatolera madengu khumi ndi awiri odzaza ndi nyenyeswa zomwe zinatsala.

Veja também