27 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ena mwa inu amene mwayima pano simudzalawa imfa musanaone ufumu wa Mulungu."
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
28 Patatha pafupifupi masiku asanu ndi atatu Yesu atanena izi, Iye anatenga Petro, Yohane ndi Yakobo ndi kukwera ku phiri kukapemphera. 29 Pamene Iye ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake, ndi zovala zake zinawala monyezimira kwambiri. 30 Anthu awiri, Mose ndi Eliya, 31 anaonekera mu ulemerero opambana akuyankhulana ndi Yesu. Iwo amayankhulana za kuchoka kwake, kumene Iye anali pafupi kukakwaniritsa ku Yerusalemu.