Pular para o conteúdo
Publicidade

Lucas 9

38 Munthu wina mʼgulu la anthulo anayitana kuti, "Aphunzitsi, ndikupemphani kuti muone mwana wangayu, pakuti ndi mmodzi yekhayu. 39 Chiwanda chikamugwira amafuwula mwadzidzidzi; chimamugwedeza kolimba mpaka kutuluka thovu kukamwa. Sichimusiya ndipo chikumuwononga. 40 Ine ndinapempha ophunzira anu kuti achitulutse, koma alephera."

41 Yesu anayankha kuti, "Haa! Anthu osakhulupirira ndi mʼbado wokhota. Kodi Ine ndidzakhala nanu nthawi yayitali yotani ndi kukupirirani? Bweretsa mwana wako kuno."

42 Ngakhale pamene mnyamata amabwera kwa Yesu, chiwandacho chinamugwetsa pansi ndi kumugwedeza. Koma Yesu anadzudzula mzimu woyipawo nachiritsa mwa mnyamatayo ndi kumuperekanso kwa abambo ake. 43 Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu.

Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake

Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake,

Veja também