Kutsatira Yesu
57 Pamene iwo ankayenda mu msewu, munthu wina anati kwa Iye, "Inu ndikutsatirani kulikonse kumene mudzapita."
58 Yesu anayankha kuti, "Nkhandwe zili ndi mapanga ake, mbalame zili ndi zisa zake, koma Mwana wa Munthu alibe malo wogonekapo mutu wake."
59 Iye anati kwa wina, "Nditsate Ine."
Koma munthuyo anayankha kuti, "Ambuye, choyamba loleni ndipite kuti ndikayike maliro a abambo anga."
60 Yesu anati kwa iye, "Aleke akufa ayikane akufa okhaokha, koma iwe pita ukalalikire ufumu wa Mulungu."
61 Koma winanso anati, "Ine ndidzakutsatani Ambuye; koma choyamba ndiloleni ndibwerere kuti ndikatsanzikane nalo banja langa."
62 Yesu anayankha kuti, "Munthu amene akulima ndi khasu lokokedwa nʼkumayangʼana mʼmbuyo, si woyenera kugwira ntchito mu ufumu wa Mulungu."