Pular para o conteúdo
Publicidade

Levítico 15

25 " Mkazi akataya magazi masiku ambiri, wosakhala pa nthawi yake yosamba, kapena akamasambabe kupitirira nthawi yake yosamba, mkaziyo adzakhala wodetsedwa nthawi yonse imene akutaya magazi, monga momwe amakhalira pa masiku ake osamba. 26 Bedi lililonse limene mkaziyo adzagonapo pa masiku onse pamene ali wotaya magazi, ndiponso chilichonse chimene wakhalira chidzakhala chodetsedwa monga mmene chimakhalira chodetsedwa pa nthawi yake yosamba. 27 Aliyense amene adzakhudza zinthu zimenezo adzakhala wodetsedwa ndipo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

Veja também