Pular para o conteúdo
Publicidade

Levitiko 24:5-9

5 "Mutenge ufa wosalala ndipo muphike makeke khumi ndi awiri ndipo keke iliyonse ikhale ya ufa wa makilogalamu awiri. 6 Muwayike pa tebulo la golide wabwino kwambiri pamaso pa Yehova mʼmizere iwiri. Mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi. 7 Pa mzere uliwonse muyikepo lubani wafungo lokoma kuti pamodzi ndi bulediyo akhale wachikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova. 8 Sabata ndi sabata nthawi zonse Aaroni aziyika makeke amenewa pamaso pa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti akhale pangano lamuyaya. 9 Chakudyacho ndi cha Aaroni ndi ana ake ndipo azidyera ku malo wopatulika chifukwa kwa iye chakudyacho ndi chopatulika kwambiri chochokera pa chopereka chopsereza cha Yehova."

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.