Yesu Achiritsa Wakhate
40 Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, "Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa."
41 Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, "Ndikufuna, yeretsedwa!" 42 Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.