Pempho la Yakobo ndi Yohane
35 Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, "Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe."
36 Iye anafunsa kuti, "Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani?"
37 Iwo anayankha kuti, "Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu."