4 Iwo anati, "Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi."
5 Yesu anayankha kuti, "Mose anakulemberani lamulo ili chifukwa chakuwuma kwa mitima yanu. 6 Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ 7 ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, 8 ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi. 9 Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse."