Bartumeyu Wosaona
46 Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. 47 Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, "Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!"
48 Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, "Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!"
49 Yesu anayima nati, "Muyitaneni." Ndipo anamuyitana kuti, "Kondwera! Imirira! Akukuyitana." 50 Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.
51 Yesu anamufunsa kuti, "Ukufuna ndikuchitire chiyani?"
Wosaonayo anayankha kuti, "Aphunzitsi, ndikufuna ndione."
52 Yesu anati, "Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!" Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.