Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 11

Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero

1 Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake 2 nati kwa iwo, "Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno. 3 Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?Kamuwuzeni kuti, Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’ "

4 Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula, 5 anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, "Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?" 6 Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite. 7 Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo. 8 Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda. 9 Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti,

"Hosana!

"Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!"

10 "Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!"

"Hosana Mmwambamwamba!"

11 Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

Veja também