42 Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama.
43 Yesu anayitana ophunzira ake nati, "Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. 44 Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya."