Mgonero wa Ambuye
12 Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, "Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?"
26 Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
Mu Getsemani
32 Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, "Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera."
Amugwira Yesu
43 Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
46 Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga.