61 Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.
Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, "Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?"
62 Yesu anati, "Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba."
63 Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, "Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso? 64 Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?"
Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa.