Yesu Ayikidwa Mʼmanda
42 Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira, 43 Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu. 44 Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale. 45 Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe. 46 Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo.