Pular para o conteúdo
Publicidade

MARKO 3

Yesu Achiritsa Wolumala Dzanja

1 Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. 2 Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. 3 Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, "Imirira, bwera kuno kutsogolo."

4 Ndipo Yesu anawafunsa kuti, "Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?" Koma iwo anakhala chete.

5 Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, "Wongola dzanja lako." Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também