22 Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, "Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda."
23 Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: "Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse. 25 Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima. 26 Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha. 27 Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera. 28 Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa, 29 koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha."
30 Ananena izi chifukwa anati, "Ali ndi mzimu woyipa."